CHRR yauza a Chakwera kuti achepetse kuyendayenda

Advertisement

Bungwe lomenyera ufulu la Center for Human Rights and Rehabilitation (CHRR) lalangiza mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera kuti achite kaye tchuthi cha maulendo awo ponena kuti ndalama zaboma zankhankhani zikusakazidwa.

Izi ndimalingana ndi mkulu wa bungweli a Michael Kaiyatsa omwe amayankhula ndi imodzi mwa mawailesi mdziko muno ndipo anati potengera ndim’mene chuma chadziko lino chilili pakadali pano, sichanzeru kuti a Chakwera adziyendayenda ngati momwe akupangiramu.

A Kaiyatsa anati maulendo ena omwe mtsogoleri wadzikoyu akumayenda ndiosafunikira kwenikweni choncho ati ndi kwabwino kuti a Chakwera akhale kaye pansi kuti dziko lino lipulumutse ndalama zomwe zikuonongedwa mmaulendowa.

Iwo ati chodabwitsa kwambiri ndichoti a Chakwera akumalimbikira kuwuza aMalawi kuti apilire pazowawa zomwe akukumana nazo chonsecho iwo akuwononga ndalama pamaulendo ochuluka akunja kwa dziko lino komaso ena mdziko mommuno.

“A Malawi akudandaula kwambiri ndimmene mtsogoleri wa dziko lino akuyendera ndipo chomwe akudandaula aMalawi sikungoyendako komano ndalama za nkhani nkhani zomwe amagwiritsa ntchito.

“Tonse tikudziwa kuti mtsogoleri wadziko akamayenda pamatengedwa ndalama zambiri. Pamakhala ndalama yamafuta agalimoto, pamafunika achitetezo komaso ma alawasi zomwe ndi ndalama zochuluka kwambiri,” atelo a Kaiyatsa.

Mkuluyu anaonjezeraso kuti maulendo ena omwe a Chakwera akumayenda opita kunja komaso mdziko muno, atha kumangotumiza nthumwi zomwe akuti zitha kuthandiza kupulumutsa chuma cha bomachi.

Nkhaniyi ikubwera pomwe mtsogoleri wa dziko linoyu Lamulungu pa 14 October wanyamuka kupita mdziko la South Africa komwe waitanidwa kukakhala nawo pachionetselo cha zamalonda mumzinda wa Durban.

Koma pomwe amanyamuka paulendowu kudzera pabwalo landege la Kamuzu ku Lilongwe, a Chakwera anati ulendowu ndiofunikira kwambiri kudziko lino ponena kuti ndiothandiza kwambiri pankhani ya zachuma

Advertisement

2 Comments

  1. Koma ndie nzoona, m’bambo ameneyu he don’t even think zaanthu mene akudandaulira, his is a failure very greedy, oziganizila yekha, May God have mercy,

  2. Chakwela ndi president okumva zake zokha komanso opanda chikondi anthu akumalawi

Comments are closed.