Sindikudziwa – Chakwera athawa funso la NOCMA

Advertisement
Malawi Economy

Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera dzulo anathawa funso lokhudza kusakazidwa kwa ndalama ku National Oil Company of Malawi (NOCMA) kudzera mu chitetezo chomwe chikuperekedwa kwa a Hellen Buluma.

A Chakwera, omwe NOCMA ili pansi pa unduna wawo wa Mphamvu za Magetsi, ananena izi pa msokhano wa atolankhani dzulo.

Ma lipoti anamveka masabata apitawa kuti a Buluma, omwe ndi wachiwiri kwa wamkulu wa NOCMA, akutetezedwa ndi apolisi ochuluka zomwe zikuononga ndalama zokwana K3.9 million pa mwezi. Zikumvekanso kuti a Buluma sakumvana ndi omwe amayendetsa Mafuta kubweretsa mdziko muno.

Atawafunsa a Chakwera za izi dzulo ku Lilongwe, iwo anati sanauzidwe bwinobwino za nkhanizi.

“Ndangobwera sanandiuze kalikonse za nkhanizi ndiye ndingotenga uphungu wanu kuti tione kuti nkhanizi zuyenda bwanji poti zikuonetsa kuti penapake sizili bwino. Ndiye ndikazimva ndikuyankhani,” anatero a Chakwera.

Msonkhanowu unakonzedwa kuti a Chakwera auze a Malawi m’mene anayendera pa ulendo wawo wa ku Kenya, Dubai ndi Scotland. Mtsogoleri wa dziko linoyu anachoka ku Malawi pa 19 October ndipo anabwera pa 6 November.

Atafunsidwa za ndalama zomwe zagwira ntchito pa ulendowu, a Chakwera anati sakudziwa koma boma lilengeza bwinobwino mtsogolomu.

Investigate Buluma, demands Malawi activists

 

Advertisement