Sand Music Festival: Makhadzi wasiya nkhani


Ngakhale phwando lamaimbidwe la Sand Music Festival latha, koma anthu akukambilanabe m’mene zinthu zina zayendera makamaka nkhani ya oyimba wa m’dziko la South Africa, Makhadzi, yemwe wasiya anthu akugundana mitu pamavalidwe ake.

Makhadzi yemwe dzina lake lenileni ndi Ndivhudzannyi Ralivhona anali m’modzi mwaoyimba akunja omwe anaimba nawo ku Sand Music Festival yomwe inachitikira ku Sunbird Nkopola ku Mangochi kuyambira Lachisanu pa 1 October mpaka Lamulungu pa 3 October, 2021.

Maimbidwe a Makhadzi anali okoma kwambiri moti anthu omwe anapita kuphwando lamaimbidweli akuyamika kuti ndalama yawo inapita mchione kaamba koti zambiri zomwe amayembekeza ndi zomwe zinaimbidwa.

Ngakhale zili choncho, anthu makamaka m’masamba a mchezo akutsutsanabe ngati mavalidwe a mzimayi oyimbayu anali a bwino potengeraso ndichikhalidwe cha anthu mdziko muno.

Makhadzi performing at the festival

Chatsitsa dzaye ndizithunzi zomwe anthu akugawana m’masamba a mchezo zomwe Makhadzi akuonetsa malo obisika zomwe aMalawi ena ati zinali zosayenera pomwe ena akuti sakuona vuto kwenikweni kaamba koti izi ndi zomwe oyimbayu anazolowera.

Anthu ambiri ayankhula pakupepesa komwe Makhadzi analemba patsamba lake la Facebook pomwe anati ndizokhumudwitsa kuti mu mzithuzi zonse, ojambula Ras Peter Kansengwa, anasankha kuika zithuzi zomwe iye anaonetsa malo obisika koma wati iye sangasinthe kavalidwe kake.

“Ndikufuna ndipepese kwaonse onditsata ngati nanuso mwakwiya ndizithunzizi. Panali zithunzi zambiri zokongola koma ojambula anasankha kuika zithunzi izi kufuna kutchukitsa kampani yake koma kuiwala kuti zikuononga umunthu wanga.

“Ndikudziwa ndine olimba ndipo zonsezi zadutsa koma pali azibale angati komaso amzanga omwe siolimba ngati ine. Mwatsoka sindingasinthe. Ichi ndi chomwe ndili ndipo ndimasangala kuti ndili chonchi,” watelo Makhadzi muunthenga omwe analemba mchingerezi.

Poyankhapo pa zomwe walemba oyimbayu, Yamikani Mazibuko anati; “Ukupepesa chifukwa chiyani Makhadzi? Asiyeni ayankhule koma zimenezo sizisintha chomwe iwe uli. ine ndiokutsatani wankulu kuno ku Malawi,”

Naye oyimba nyimbo zauzimu mdziko muno, Onesimus sanapsatile mau ake koma kumulimbikitsa Makhadzi kuti asafooke; “Ndiwe otchuka Makhadzi, palibe chomwe chingakutsitse pansi.

Mbali inayi Yamikani Thomson anati; “Uyuyu asadzabwereso kuno chifukwa mavalidwe ake sakugwirizana ndichikhalidwe chathu, osamasekelera zopusa,”

Ndipo m’modzi mwa akuluakulu omwe amakoza mwambowu a Lucius Banda, adzudzula Ras Peter Kansengwa yemwe anajumbula zithunzi zomwe zikugawidwazi ponena kuti uku ndikubwezeretsa mmbuyo ntchito yopititsa patsogolo ntchito yokopa alendo.