Phwando ku Joweni: Chakwera atenga mudzi onse kumka nawo kunja


Ulendo wa mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera omwe anapita mu dziko la South Africa wamezedwa ndi nkhani za mneneri othawa Shepherd Bushiri. Nkhani ina yabisika ndi ya chinamtindi chimene a Chakwera ananyamula pa ulendowo.

Malingana ndi malipoti ochoka mu dziko la South Africa, a Chakwera anapita m’dzikolo ndi anthu ena 64. Ulendowo anakangogona tsiku limodzi.

Malinga ndi nduna yoona za md’ziko mu dziko la South Africa, a Aaron Motsoaedi, ulendowo unasokolotsa khamu la anthu omwe ena anakamuchingamila Chakwera ndi mayi wa fuko lino, a Monicca Chakwera, pomwe ena sakudziwika kwenikweni kuti amakatani.

“Tsiku lonyamuka a Chakwera kunabwela anthu 65 pa bwalo la ndege la asilikali la Waterkloof,” anatelo a Motsoaedi, “onsewa amafuna anyamukile pabwalo’lo zomwe sizinali zotheka.”

Pa tsiku lenileni limene a Chakwera anafika mu dziko la South Africa, ndege yomwe anachita hayala n’kuti itanyamula anthu 19 okha kuphatikizapo iwo ndi akazi awo. Koma nthawi yonyamuka n’kuti mudzi uja utakula katatu ndi kuonjezelapo ena a banyila.

Adindo a mu dziko la South Africa anakana kuti anthu enawo asakwele nawo ndegeyo chifukwa sanafike limodzi ndi mstogoleri wa dziko lino’yu. Izi zinakwiyitsa anthu ena pamenepo makamaka a Eisenhower Mkaka, a nduna yoona za ubale wa Malawi ndi mayiko ena, omwe anatsogola ndi anzawo ena.

“Pa malamulo sitikanawalola, pa bwalo la Waterkloof sipokwelela aliyense ndege,” anatelo a Motsoaledi.

A Motsoaledi ananenanso kuti pa anthu 19 anabwela ndi a Chakwera aja, awili anasalila mu dziko la South Africa lomwelo ndipo sanabwelele nawo a Chakwera. Atafunsidwa kuti awiliwo anatsala kuti azitani, iwo ananena kuti panalibe chodabwitsa.

“Alendo akabwela amapezekapo otsalila kuti mwina agule zinthu, mwina aone achibale, ndinso kuti ena amakhala ali ndi nyumba kom’kuno. Amabwelela nthawi yawo ikakwana,” anatelo a Motsoaledi.

Chimene chadabwitsa anthu ndi choti mu nyengo imene chuma cha Malawi chikudandaulidwa kuti chaombedwa ndi matenda a Covid, boma latsopano la a Chakwera likunka kuononga ndalama ndi kutenga namtindi wa anthu kupita nawo ku mayiko akunja komwe zokambilana zake ndi zoti atha kuchita pa Zoom monga akuchitila atsogoleri ambili.

“Ngati mukutengana gulu chonchi pa Joweni pomwepa, ku UNGA ndiye muzatani?” anadabwa choncho a Malawi ena pa masamba a mchezo a Facebook.