Afika Atcheya, ati muvotele DPP ndi UDF

Advertisement

Lonjezo linadulitsa mutu wa Yohane. Atcheya Bakili Muluzi kukhala ngati sakufuna anthu adule mutu wa mwana wao Atupele.

Patangodutsa masiku Atupele Muluzi atauza anthu a ku Zomba kuti Bambo ake a Bakili Muluzi akubwela kuti apeleke moni, a Bakili ayambapo kumema anthu kuti azavotele zipani za DPP ndi UDF pa masankho akubwelawa.

Mu vidiyo imene anthu akugawana, a Muluzi ali mmudzi mwa Kapoloma mmene akuuza anthu kuti poponya voti awapatse a Mutharika.

“Tithokoze a Professor posankha mwana wa pompano kuti akhale wachiwiri wawo,” akutelo a Muluzi.

Iwo akumamveka akupitiliza kuti zatelemu ndiye kuti anthu a ku chigawo cha kummwela kwa Malawi avotela DPP imene yagwilizana ndi UDF.

“Kuno ku Machinga, Mangochi, Balaka ndi Zomba ndiye kuti voti yathu ndi DPP,” akutelo a Muluzi.

Advertisement