Uheda Matumba koma suwinabe – Chimulirenji sanathane ndi Chilima

Advertisement

Yavuta nkhondo ya a Ngoni a mu Ntcheu. Onse anakhalapo oyenda ndi Peter Mutharika.

Patangopita masiku ochepa a Saulos Chilima atadzudzula a Mutharika kamba kongogwilitsa ntchito a Everton Chimulirenji pa chisankho cha 2019, a Chimulirenji adayankha ku Dedza. A Chimulirenji ananena kuti a Chilima ndiwo anapanga upo owachotsa pa udindo wachiwili kwa mtsogoleri wa dziko.

Koma zikuoneka kuti nkhondo ikupitililabe pamene a Chimulirenji apitiliza kunyogodola a Chilima.

Pa msonkhano omwe unachitika ku Masintha mu mzinda wa Lilongwe, a Chimulirenji ananyodola a Chilima kuti sawina zisankho ngakhale agwilizana ndi a Chakwera a chipani cha Kongeresi.

“Akulimbana ndi ine chifukwa chani?” anafunsa motelo a Chimulirenji. “Inetu ndi wa DPP ndipo mpaka ndizafa ndili ku DPP.”

Iwo anapitiliza ndi kunena kuti DPP ipambana masankho amene akuyembekezeka kuchitika pa 23 June.

A Chimulirenji, omwe owakonda amawatcha a Dzonzi, anapezaponso mwayi oti anyogodole a Chilima.

“Chaka chatha ankapanga zodumphadumpha pa nsanja, chaka chino ndiye akuheda matumba. Komabe sawina,” anatelo a Chimulirenji.

“Ndipo olo ahede mipira pa msonkhano sikuti awina iyayi,” anatsindika a Chimulirenji.

Pa nthawi imene a Mutharika amasankha a Chimulirenji ndi kuti a Malawi ambili asakuwadziwa bwinobwino ndipo anthu akhala akuwanena kuti ndi ofatsa.

Advertisement