A Mtambo akufunidwa ndi apolisi

Advertisement

Apolisi akusakasaka a Timothy Mtambo omwe miyezi yapitayo anauza anthu kuti anawankha chipolopolo cha apolisi.

A Mtambo, omwe ndi mkulu wa bungwe lomenyera ma ufulu la HRDC, akufunidwa kamba ka ganizo lawo lofuna kupanga zionetsero pa 25 March zokathera ku nyumba ya boma ku Lilongwe zomwe akuti ndi zofuna kukakamiza mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika kusaina ma bilo omwe nyumba ya malamuo inavomereza mwezi watha.

Apolisi akuti kupanga zionetsero ku nyumba ya mtsogoleri wa dziko lino ndi kosaloledwa ndi malamulo ndipo kumemeza anthu kuti aphwanye malamulo ndi kosaloledwaso.

Padakali pano, a polisi amanga wachiwiri kwa a Mtambo a Gift Trapence komamnso membala wa gululi a Macdonald Sembereka.

Kumangidwa kwa akuluakuluwa kwadza dzulo patatha malo ochepa mtsogoleri wa dziko lino a Mutharika atauza a polisi ndi asilikali ankhondo kuti azapange chilichose chotheka kuletsa ochita zionetserowa kukafika ku nyumba ya boma.

A Mutharika anachenjezaso a Mtambo kuti iwo sangakhale wamkulu kuposa boma. A Mutharika ananenaso kuti atopa nid zionetsero zomwe a Mtambo amapangitsa

 

Advertisement