Malonda athu sakuenda, tikufuna tikambirane ndi a HRDC asiye zionetsero – Leston Mulli

Advertisement

M’modzi mwa anthu amalonda m’dziko muno a Leston Mulli ati ndiokhudzidwa kaamba kakusokonekela kwa ntchito za malonda chifukwa cha zionetsero m’dziko muno ndipo akambirana ndi a mabungwe kuti asiye zionetsero.

A Mulli amalankhula izi pansonkhano wa atolankhani lachiwiri mu mzinda wa Blantyre komweso anati zomwe zikuchitikazi ndizokhumudwitsa maka kwa aliyese ochita malonda ku Malawi kuno.

Mkulu wa zamalondayu anati kupatula kusayenda bwino kwa malonda, chokhumudwitsa china ndi choti anthu azionetserowa akumaba komaso kuononga katundu wa ndalama za nkhaninkhani wa anthu omwe sanalakwe kali konse.

Iwo anati apanga zothekera kuti pamodzi ndi akuluakulu ena pankhani za malonda mdziko muno akumane ndi anthu omwe akutsogolera zionetserozi kuti akambilane ndicholinga choti malonda m’dziko muno ayambeso kuyenda bwino ngati kale.

“Ma bizinezi m’dziko muno asokonekera ndipo izi zithaso kupangitsa kuti anthu akunja opanga malonda omwe amabweretsa ndalama m’dziko muno asiye kuchita malonda chifukwa aziona kuti ku Malawi zinthu zisikuendako bwino, Kodi tikhalire zimenezi?

“Mwaonapo a Bakili Muluzi anawaitana a HRDC ndi kukambilana nawo koma zakanika. Ifeso tikufuna tiwaitane tikambilane nawo tiwauze kuti ifeyo anthu othandiza kupanga ndalama komaso mwayi wa ntchito, tikuvutika chifukwa zinthu zathu sizikuenda,” anatero Mulli.

Iwo anati zomwe zikuchitikazi zikumaonetsa kuti amene akumatsogolera zionetserozi ali ndi zifukwa zawo zawo zomwe akupangira izi ndipo ati izi sizikuyenera kukhala choncho ponena kuti, zionetserozi zikupangitsa kuti chuma cha boma chisokonekere.

A Mulli anapitiliza kunena kuti ndizodabwitsa kuti akuluakulu a HRDC akufuna kuti mkulu wa bungwe loyendetsa zisankho la MEC a Jane Ansa atule pansi udindo wawo pomwe nkhaniyi ili ku bwalo la milandu.

Iwo anafunsa kuti nanga mai Ansa atatula pansi udindo wawo lero, sazafunika kuti apelekere umboni pa mulandu omwe uli kukhothiwu?

Posachedwapa, mkulu wa bungwe la HRDC lomwe likupangitsa zionetserozi a Timothy Mtambo, anatemetsa nkhwangwa pamwala kunena kuti iwo sasiya kupangitsa zionetselo mpaka mai Ansa atule pansi udindo wawo.

Koma ngakhale zili chomcho, sabata ino zionetsero zomwe zimayembekezeka kuchitika lachiwiri komaso lachinayi, sizinachitike.

Advertisement