Siyani nkhanza kwa amai – nduna iwuza otsogolera zionetsero

Advertisement

Nduna yowona kuti pasamakhale kusiyana pakati pa amayi ndi abambo pa ntchito, a Mary Navitcha, apempha kuti azitsogoleri a mabungwe omenyera ufulu wa anthu mdziko muno asiye kuchitira nkhanza azimayi.

Mai Navitcha amalankhula izi pazionetsero zomwe zinachitika lachitatu mu mzinda wa Blantyre poikila kumbuyo wapampando wa bungwe la MEC a Jane Ansa kuti asatule pansi udindo wawo monga momwe amabungwe ena akufunira.

Kuzionetseloku komwe kunali chinantindi cha azimayi, ndunayi inati sizoyenera kuti azitsogoleri a mabungwewa azinyoza azimayi ngati momwe akuchitila ndi mai Ansah ndipo anati unduna wawo uyesetsa kuti mchitidwewu utheretu.

Iwo anati nthawi yakwana kuti azimayi mdziko muno alemekezedwe. Anaonjezera kunena kuti zomwe akupanga amabungwewa kunyoza mai Jane Ansah ndinkhanza ndipo anapempha amabungwewa kuti asiye.

“Nthawi yakwana tsopano, amai alemekezedwe. Ndipemphe amabungwe ndipemphe azipani kunena kuti asiyiletu kunyoza azimayi. Simukunyoza mzimayi chifukwa chantchito yomwe alinayo, koma akumunyoza chifukwa cha mmene anabadwira, maonekedwe ake, mbiri yake ngakhale banja lake.

“Zimenezi sizikupatsa ulemu ngati dziko loopa Yehova ngati dziko lamtendere. Nde tikunena kuti Dr Jane Ansah sakutula pansi udindo chifukwa chotukwanidwa kapena kunyozedwa. Ngati Dr Ansa analakwa khothi lidzalamula kuti iwo analakwa koma ife tikukana kuweruziratu.” Atero a Navicha.

Pophera mphongo pa zomwe anena a Navitcha, mtsogoleri wa bungwe lomwe linakonza zionetserozi la Forum for Concerned Women in Malawi a Seodi White anati azimai nawo akufuna kupatsidwa ulemu ngati munthu aliyese.

Mai White anati vuto lomwe lilipo ku Malawi ndiloti pakakhala nkhani yomenyera ufulu wa amai, a mabungwe omenyera ufulu amafuna kuti nkhaniyi ifafanizidwe zomwe anati ulendo uno bungwe lawo sililora kuti zichitike.

“Ife amene takhala tikulimbikitsa zothetsa nkhanza kwa amai mdziko muno timadziwa kuti munthu akabweretsa chinthu chofuna kutsutsa mchitidwe wankhanza kwa amai, anthu amafuna kuti nkhaniyo ayifafanize kuti ukhale ngati amene ukuyambitsawe ndiwe wamisala.

“Izi taziona ndipo aka sikoyamba, tinapanga zionetsero zoyamba zonga izi mchaka cha 1999 ndipo amatinenaso chimodzimodziso kuti ndife azimai amisala lero akunenaso chimodzimodzi koma ife tikuti izi ndinkhanza kwa amai ndipo zither,” anatero a White.

Pakadali pano zipani komaso mabungwe omwe amapangitsa zionetsero zokakamiza mai Ansah kutula pansi udindo wawo ati sasiya kupangitsa zionetserozi mpaka a Ansah atatula pansi udindo wawo.

Iwo adzudzula a Ansah ponena kuti analephera kuyendetsa bwino zotsatila zachisankho.

Advertisement

One Comment

  1. Makamaka atumbuka vinyawu vachabechabe mukupita pamsewu nkumakawabela anthu mmalo mogwila ntchito yoti ikupindulireni. Osazimvela chisoni anthu otsalira ngati inu mukuotcha katundu wa boma chakuthandiza nchani? Mapeto ake panopa akutsrjelani mchitolokosi ambuli inu! Naye at Trampece ndi Sembeleka mwapindulanji pakuganyula kwanu kkkkkkkkkk

    Koditu kholo sililichitila mwano ayi, limakusungila mtaji nthawi yausiku pokagona at the end umakagona kunja anzako amakupusitsa masana aja atagona mnyumba. Inu awirinu pano tikunena pano mulikukhaula mmanja mwa apolice kkkkkkk

Comments are closed.