A Chimulirenji anyula: ati APM anamwalira 2012

Advertisement

A Everton Chimulirenji omwe ndiwapambuyo pa mtsogoleri wa DPP a Peter Mutharika pa zisankho za mwezi wa mawa agwedeza masamba a mchezo.

Mu kanema yomwe siinasiye malo mmagulu ocheza pa WhatsApp komaso Facebook, bambo Chimulirenji akuoneka akunena kuti yemwe ndi mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika anamwalira muchaka cha 2012.

Kanemayi ikuonetsa a Chimulirenji ataima pa nsanja akulankhula pa umodzi mwa misonkhano yokopa anthu yomwe chipani chawo chapangitsa posachedwapa.

Iwo awoneka akujejema polankhula ndipo anauza anthu omwe anasonkhana pamalopa kuti chipani cha DPP chinayamba kulamulira dziko lino mchaka cha 2009.

M’modzi mwati akulu akulu achipanichi ndiomwe anawakoza ndikuwauza kuti DPP inatenga ulamuliro mu 2004 osati 2009.

Yemwe akuyembekezeleka kuzakhala wachiwiri kwa mtsogoleri wa dzikoyu anapitiliza kulakwitsa ponena kuti muchaka cha 2012 chipani chawo chinaonekeledwa zovuta pomwe chinataya mtsogoleri wake.

A Chimulirenji mmalo monena kuti otisiyawo anali malemu Bingu Wa Mutharika, iwo anatchula mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika.

“Chipani cha DPP chinayamba kulamula dziko lino muchaka cha 2009. Ndipo titafika mchaka cha 2012, tinaonekeledwa ngozi ya professor Arthur Peter Mutharika. Mzimu wawo uuse mu mtendere,” anatero a Chimulirenji mukulakwitsa kwawo.

Pakadali pano, kanemayi yakoka ndemanga zonyoza komaso zitonzo zochuluka pa mkuluyu pomwe anthu akupitiliza kuikambila mma gulu ochuluka pa tsamba la mchezo la Facebook komaso WhatsApp.

Advertisement