Njoka iba K70 miliyoni mu ofesi

Advertisement
Naira

Ndalama yokwana K72 miliyoni yasowa mu ofesi la bungwe loyang’anila za mayeso ndipo atafunsidwa munthu amene amayenela kuteteza, iye wati yasowetsa ndi njoka.

Zochitika ku Africa ndi zodula mutu ndithu, zoopsa ndi zopatsa nthumanzi.

Naira
Ndalama yokwana K72 miliyoni yasowa mu ofesi la bungwe loyang’anila za mayeso ku Nigeria.

Malipoti ati mu dziko la Nigeria, Mayi wina oyang’anila chuma ku bungwe la mayeso a mu dzikolo wadabwitsa anthu ndi nkhani yoti chinjoka chasowetsa ndalama za nkhani nkhani.

Ati ku ofesi ya mayiyo kunabwela akulu akulu a za kafukufuku ofuna kudziwa mmene chuma chikuyendela.

Mukufufuza kwawo, anapeza kuti chuma chinasokonekela ndithu chokwana 72 miliyoni mu ndalama ya ku Malawi kuno.

Iwo atafunsa Mayi amene amayenela kusamala ndalamazo ati anawauza mmaso muli gwa kuti ndi njoka yomwe yatenga ndalamazo.

Koma a bungweli ati nkhaniyi ndi mbwelela ndipo pano ayimitsa pa ntchito munthu amene amayenela kuteteza ndalamayo.