Nyerere zafakidwa mpweya wa fodya uku

Advertisement
Carlsberg Cup

Awatibulanso. Kachikena awatsambitsa madzi a matope. Ku Bingu anapita akusangalala kuja, Manoma atuluka ndi nkhope zozyolika akulila mayomayo.

Pa masewero amene anakodola khamu, maule lero aliritsa nyerere kachikena atazitsomphola chikho cha Carlsberg.

Anali masewero oyamba ndi pakalapakala. Nyerere ndizo zinayamba kumwetsa chigoli kudzera mwa mnyamata wakale wa Bullets Jafali Chande.

Panangotha mphindi khumi kuti maule abwelelemo pamene nawo anaikamo chawo kubweletsa masewero pa 1 – 1.

Koma nyerere zinapangabe makani ndipo patatsala kanthawi pang’ono kuti chigawo choyamba chithe, zinakodolelamo china kuika masewero pa 2 – 1.

Mu chigawo chachiwiri, nyerere zinayesetsa ndithu kuti ziteteze golo lawo koma zinali chabe pamene maule nawo anabwela ndi kukodolelamo china kuti afikitse masewero pa levulo.

Pokutha pa mphindi 90, matimu onse anali atafanana mphamvu ndipo anajowela ku gawo la ma penate.

Uko ndiko nyerere zinaona mbonaona pamene mnyamata wawo Yamikani Chester anaphonya kuwasiya a Bullets akuyimba njira yonse.

Advertisement

2 Comments

  1. Kungoti nchizolowezi cha Anoma kuluza pamaule mwina pang’ono anangoiwalisa ndi bus ipite komano zinazo ndiye mbola yeni yeni. Nanga team yomakhala 6yrs osawina mu tnm ligi ndiye leronso ndi izi shammmmmmmmmme

Comments are closed.