Nyerere zija azisasantha, azisambwadza ndi kuzisiya kukamwa kakasi

Advertisement
Carlsberg Cup

Mankhwala a nyerere adziwika tsopano, ndi fodya wa Nyasa.

Nyerere za manoma zachoka pa Bingu National Stadium zikulila chokweza, a neba awo a Bullets atawatibula masana dzuwa likuswa mtengo.

Malawi football
Nyerere zija azisasantha

Pa masewero amene anakodola khamu, nyerere ndizo zimaoneka ngati zipambana potengela kuti chaka chino zawo mu ligi zikukhala ngati zasongola. Malinga ndi kuvutika kwa Bullets, ambiri amakhulupirira kuti pokutha pa tsiku, nyerere zikhalanso zikumwa wa mkaka.

Koma timu ya fuko ya Bullets yangotsimikiza mbiri yoyambila 2012 yoti zivute zitani koma ku ligi, nyerere ndi akazi awo basi.

A Bullets anaoneka a njala yofuna chigoli ndipo njala yawo inaphelezela mu chigawo choyamba chomwe pamene mnyamata wawo Emmanuel Zoya anamalizitsa mpira ochokera kwa Chiukepo Msowoya kuti ukagwedeze ukonde.

Chinali chigoli choyamba cha masewelowo ndipo chotsiriza chinalinso chomwecho.

Manoma anayesela umu ndi umu kuti agoletse koma popanda zawo zokodzela pagolo zija, mpira unakanika kuthela mu ukonde. Ngakhale anasintha osewela ena, palibe chime
chimene anapindula.

Pokutha pa masewero, Bullets inali ikuyimba olire olire pamene nyerere zinali zikulila.

Padakali pano, Bullets ndi nyerere akusiyana ndi ma pointi seveni basi.