‘Kulidi katangale kuno?’ boma la a Mutharika likukayika

101

Zonse zija zoti a Malawi ochuluka akunyema pamseu, zoti akunyema pofuna ziphaso zoyendela (passport) ngakhale za u dalayiva, Boma la Malawi likukayika zoti kuli katangale.

Mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika amene nduna yawo ya za malimidwe yakale a George Chaponda anachotsedwa pa udindo powaganizila kuti amafuna kuchita za katangale, lero akhala akutsegulila msonkhano wofuna kudziwa ngati zili zoona zoti mu dziko muno muli katangale.

Msonkhanowu ukuchitikila mu mzinda wa Lilongwe. Bungwe lothetsa mchitidwe wa katangale mu dziko muno la ACB mogwilizana ndi unduna wa za Chilungamo ndiwo akonza msonkhano umenewu.

Malinga ndi uthenga ochoka ku boma, ati msonkhano umenewu ukufuna kutsimikiza ngati katangale akuchitikadi mu dziko muno kapena anthu angokokomeza.

Pa msonkhano umenewu umene anthu ena audzudzula kuti ndi chibwana chabe, aitana namandwa wa mu dziko la Kenya kuti azayankhulepo.

Share.
  • Opinion