9 November 2016 Last updated at: 6:50 PM

Zivuta ku Sunagogi pamene Mai Clinton aluza zisankho

Zisankho za mu dziko la Amereka zasokoneza utumiki wa mkulu wa ku Nigeria otchuka ndi nkhani za ulosi, a TB Joshua.

Lachiwili pa 8 November anthu anavotela Bambo Donald Trump kuti ndiye akhale mtsogoleri wa dziko la Amereka akachoka a Barack Obama chaka chamawa.

TB Joshual Hillary Clinton Donald Trump US Elections Nigeria

Zamuvuta Joshua

Kupambana kwa Bambo Trump kwasokoneza mitu anthu ambiri amene amayesa kuti a Mayi Hillary Clinton apambana. Mayi Clinton amene anakhalapo ndi udindo mu ulamulilo wa a Obama amaoneka a chikoka ndi okondedwa.

Chikoka chawo chinasokoneza mutu mtumiki wa Mulungu TB Joshua mpaka anapanga ulosi oti Mayi Clinton apambana.

“Ambuye wandionetsela za zisankho za mu dziko la Amereka,” anatelo Bambo Joshua amene ananenelapo za imfa ya mtsogoleri wa kale wa dziko lino a Bingu wa Mutharika.

“Ine ndikuuzeni kuti Ambuye akuti apambane ndi mzimayi,” Bambo Joshua ananetelo uku owatsatila akutchaya ma Ameni.

Koma zotsatila za zisankho zitatuluka, a Joshua anapezeka kuti ananama.

“Wawina zisankho ndi munthu wammuna, iwo aja bwanji amati azakhala wamkazi?” anafunsa choncho anthu odabwa.392 Comments On "Zivuta ku Sunagogi pamene Mai Clinton aluza zisankho"

Leave a Reply

 
MwanaMwa
Lilia's Weekly Dose
 
Whats-Hot
 
OPINION