Mkwatibwi athawitsa ndalama za pa pa ukwati

Advertisement
Money currency

Mkwati wina m’dera la mfumu Musisita m’boma la Nkhotakota walira ching’ang’adzi mkazi yemwe adakwatira naye atathawa ndi ndalama zomwe adapeza patsiku la ukwati wawo.

Malingana ndi mfumu Masisita, Bamboyu adakwatirana ndi mayiyu mulungu wathawu koma bamboyu adazizwa ataona kuti mayiyu pamodzi ndi ndalama zomwe adapeza patsiku la ukwati wawo sizikuoneka.

“Padali patangotha masiku awili pomwe mkuluyi adadziwa kuti mkazi wake wamuyenda njomba pozembetsa ndalama nkuthawa nazo,” Mfumu Musisita Wauza Malawi24.

“Bamboyo adayesa kufufuza komwe kuli mkazi wakeyu koma mpaka pano sakukupeza,” adaonjezela mfumu Musisita.

Money
Ndalama zathawisidwa.

Mkwati ndi Mkwatibwiyu onse ndi a m’mudzi mwa mfumu Musisita, Mfumu yayikulu Kanyenda m’boma la Nkhotakota.

M’mudzi omwewu wa mfumu Musisita, M’busa wina wasiya ubusa kamba kosankha kukhala ndi mkazi wachiwiri.

Malawi24 yapeza kuti m’busayi yemwe ndi wa mpingo wina m’dera lamfumu Musisita m’boma la Nkhotakota adakwatira mkazi wachiwiri zomwe zidali zotsutsana ndi malamulo a mpingo wake.

Malipotiwa akusonyezaso kuti izi sizidasangalatse akuluakulu ampingowo omwe adamufunsa m’busayi kuti asankhepo chimodzi pakati pomusiya mkazi wachiwiriyo ndikupitiliza ubusa kapena kusankha mkaziyo ndikusiya ubusa.

Akuluakulu ampingowa adazizwa ataona kuti m’busayi wasankha kusiya ubusa ndikukhalabe ndi mkazi wachiwiriyu.

Pakadali pano m’busayu wanenetsa kuti sangamusiye mkaziyu wake wachiwiriyu.