21 October 2016 Last updated at: 12:46 PM

Boma lipemphedwa kuti lizimanga onse onama pa FACEBOOK

Inu nonse amene mukutchukitsa kuti mtsogoleri wa dziko lino akudwala ndipo akuganiza zotula pansi udindo, akuti muzimangidwa.

Anthu ena omenyela ufulu wa anthu wa chibadwidwe ndiwo apempha boma la Malawi kuti liyambe kuunika bwino nkhani zimene anthu amaika pa Facebook ngakhaleso mu ma WhatsApp.

Billy Banda

Billy Banda: Boma libweretse lamulo latsopano

“Anthu akuchulutsa bodza pa Facebook ndi pa WhatsApp, papezeke njira yowalangila anthu onse abodza,” anatero a Billy Banda amene m’mbuyomu anali patsogolo kumenyera ufulu wa anthu.

Iwo anagwilizana ndi a Undule Mwakasungula amene nawo anapempha kuti boma lithetse chibwana pa Facebook ndi pa WhatApp.

“Anthu akumangonena bodza basi, pakufunika malamulo okhwima oti azilanga anthu otelewa,” a Mwakasungula anatelo.

A Banda ananena kuti m’mene anthu amanenela za umoyo wa mtsogoleri wa dziko lino panthawi imene anali ku America kunali kongoyenela kuti ena alangidwepo basi.

Anthu anatchukitsa kuti a Mutharika akudwala pa nthawi imene anatchona mu dziko la America, ena anati atsogola ndithu. Pamene a Mutharika anabwela dzanja lawo lamanja liri looneka lopuwala ena anati a Mutharika angobwela ngati chiphimba mmaso ndipo usiku atengedwa kumka ku chipatala.463 Comments On "Boma lipemphedwa kuti lizimanga onse onama pa FACEBOOK"