Mafunso a komwe kudapita lamya ina ya malemu Saulos Chilima amanga nthenje tsopano pomwe mboni ya chisilikali yati idawona mafoni atatu osati awiri okha.
Lachitatu madzulo, Major General Richard Chagonapanja adawonekera ku komiti yapadera yomwe ikufufuza za ngozi yandege yaku Chikangawa pa 10 June, 2024.
Major General Chagonapanja adauza komitiyi kuti iye ndiamene ankatsogolera a silikali a Malawi Defense Force (MDF) pa ntchito yosakasaka ndege ya Dornier.
Muumboni wake, Major General Chagonapanja watsindika kuti pa 11 June, 2024, tsiku lomwe ndegeyi idapezeka ku Nthungwa, adawona ma foni a mmanja atatu a malemu Chilima.
“Chidwi changa chinali pa katundu wa a Chilima. Anthu akukamba kwambiri za lamya ziwiri zokha koma ine ndinaona lamya zitatu,” watero Major General Chagonapanja.
Chagonapanja wati pa mafoni omwe adawonawa, lamya imodzi imaoneka kuti munthu utha kugwiritsa ntchito, pomwe wati ina inali yosweka pang’ono pa galasi, ndipo ina inali yosweka kwambiri.
Pakhota nyani mchira mpakuti mkazi wa malemu Chilima, Mary adauza komitiyi kuti adapatsidwa ma foni awiri okha omweso adati anali ophwanyika kwambiri.
“Patadutsa mwezi ndipamene tinadzapatsidwa ma foni awiri ophwanyika. Koma ndikuona ngati ikutsala imodzi, ngakhale kuti sindingatsimikize, koma ndikuganiza kuti adali ndi mafoni atatu,” adatero Mary muumboni wake.
Malemu Chilima adafa pa ngozi ya ndegeyi pamodzi ndi anthu ena asanu ndi atatu pomwe ankapita ku maliro a loya Ralph Kasambala.
