Mtsogoleri wa chipani cha UDF, Atupele Muluzi wati amalemekeza kwambiri m’tsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika koma wati ndikofunika kuvomereza kukula kwawo.
Muluzi wanena izi pamene amacheza pa wayilesi ya kanema ya Zodiak, nkati mwa pulogalamu ina.
“Ine ndine m’modzi amene ndinagwira ntchito ndi President Professor Arthur Peter Mutharika, ndagwira nawo ntchito dzaka ngati Nduna, I respect him, I love him, koma munthu ukakula umayenera kuvomereza”, adatero a Muluzi.
Muluzi watinso utsogoleri komanso zaka za m’tsgoleri ndi zina mwa zinthu zimene zikupangitsa anthu ena kutengerapo mwayi wopanga zomwe akufuna m’dziko muno.
Iwo ati ndikofunika kudziwa bwino za mmene zinthu m’dziko muno zikuyendera chifukwa ngati pali vuto, m’dziko muno muli wachiwiri kwa mtsogoleri amene anasankhidwa ndi malamulo kuti akuyenera kuthandizila m’tsogoleri.

Muluzi wati zimene zikuchitika kuti mtsogoleri ndi wachiwiri wake palibe ubale wabwino ndi zinthu zosakhala bwino ndipo zikubweretsa mafunso za momwe dziko lino likuyendera.
Popeleka ganizo lawo pamene dziko lino latha chaka chiponyereni voti pa zisankho zapitazo, Muluzi wati bomali likuyesetsa koma mavuto alipo.
A Muluzi ati mavuto monga katangale akuchitika chifukwa pakusoweka utsogoleri ndipo a Malawi akuyenera kuzifunsa kuti m’tsogoleri wawo alikuti?
Iye wati sipikala wa Nyumba ya Malamulo, Sameer Suleman anafotokoza kuti zinthu zambili zikuchitika koma pano palibe chomwe chikuwonekanso chokhudzana ndi nkhaniyi, ndipo pakuyankhula kwawo a Muluzi, akuti pali vuto ndi utsogoleri.
