Wophunzira wina pa sukulu yaukachenjede ya University of Malawi (UNIMA) amafuna kuchotsa moyo wake posowa mtendere ndi ngongole ya pafupifupi K600,000 yomwe akukanika kubweza.
Joseph Nenani Major, yemwe ali m’chaka chachitatu, wati wakhala akubwereka ndalama kwa anthu angapo kuti adzithandizire pa maphunziro ake.
Iye wati chili chonse chokhudza maphunziro ake amadzipangira yekha choncho anabwereka K594,500 kwa anthu anayi.
Pomwe eni ndalamazi akuzifuna, iye alibe mtengo wogwira, zomwe zakhala zikumusowetsa mtendere mpaka zinamukankhizira kupanga chiganizo chodzipha.
M’kalata yomwe analemba, Major wati m’mbuyomu anachotsedwapo sukulu kawiri chifukwa cha ngongole ndipo amayenera kumaliza maphunziro ake mchaka cha 2021/22.
Major yemwe amachokera m’mudzi mwa Meja m’boma la Chikwawa wati anzake ndiomwe anathamanga ndikulepheretsa choipachi.
Gawo 229 la malamulo ozengera mirandu (Penal Code) limati munthu ofuna kudzipha amayenera kulandira chirango chokhala kundende zaka zosapitirira ziwiri.
,
