Tingovomereza, n’kayankhule zambiri sizikhala bwino — Mtetemera


Img 20260919 Wa0033- Malawi24

Mphunzitsi wa timu ya Mighty Wanderers, Macdonald Nginde Mtetemera wasankha kusayankhula zambiri zomwe zikupangitsa timu yake kusachita bwino mmasewero angapo apitawa.

Mtetemera yemwe akugwirizira ntchito ya m’phunzitsi wamkulu kutsatira kuchotsedwa ntchito kwa Bob Mpinganjira, anavomereza kuti pakadali pano zinthu sizikuwoneka bwino kumbali ya Manoma.

Mphunzitsiyu amayankhula izi pa Nankhaka, masana a loweluka pomwe timu yake inagonja kwa Blue Eagles ndi zigoli ziwiri kwa chimodzi, mu FDH Premiership.

“Sizinayende kutengera zotsatira, koma kuti ndiyankhule zambiri sizikhala bwino, tingovomereza” anatero Mtetemera.

Ngakhale timuyi yagonja, koma Mtetemera anawonetsa kukondwa ndi mmene timu yake inachitira muchigawo chachiwiri.

Iye anati wazindikira vuto lakusagwirizana kwa otseka kumbuyo ake omwe akumapangitsa kuti timuyi idzichinyitsa zigoli zopeweka, ndipo wati akonza vutoli chisanayambe chigawo chachiwiri cha mpikisanowu.

Zateremu Mighty Wanderers yalephera kumaliza pamwamba pa ndandanda wamatimu mu gawo loyamba, pomwe tsopano yamaliza pa nambala yachitatu ndi mapoint 29, ndipo Blue Eagles ndiyomwe ikulamulira mndandanda ndimapoint 31 pamene FCB Nyasa Big Bullets ndiyachitatu itapeza mapoint 30.

Kugonja uku ndikwachinayi motsogozana kumbali ya Manoma, kutsatiraso kufa ndi Ekhaya FC mu Airtel Top 8 komaso Simba kawiri mu CAF Champions league.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading