Maso a MCP alunjika ku 2030


Chikondi Kampachike Chisale- Malawi24

Podziwa kuti kutola khobwe ndi m’mawa, chipani chotsutsa cha Malawi Congress Party (MCP) chachilimika pa ntchito yokozaso zinthu mchipani pomwe chikukhumbira kudzatengaso boma pa chisankho cha mu 2030.

Mwazina, chipanichi pano chagawa zigawo zosiyanasiyana zatsopano, kuphatikizapo chigawo cha Bua chomwe chili ndi maboma a Ntchisi, Dowa komanso Kasungu.

Phungu wa dera lapakati m’boma la Kasungu Chikondi Kampachike Chisale watsimikiza za izi kudzera m’kanena yemwe wayika pa tsamba lake la mchezo la Fesibuku.

Malinga ndi Chisale Kampachike, emwenso ndi m’modzi mwa anthu omwe akuyimira nawo ngati wapampando wa chigawochi, wati chipanichi chachita izi pofuna kuti chipitilire kukhala cha mphamvu.

“Cholinga cha chipani pogawa mphamvu zimenezi ndi choti chipani chipitlire kukhala cha mphamvu, tithe kufikira anthu m’madera osiyanasiyana kunkhani yomema anthu kuti akalembetse mavoti,” anatero Kampachike.

Iye wati izi zithandizira kuti mchipanichi mukhale chimvano cha mavu komaso kuti athe kuteteza voti yawo.

Malinga ndi Chisale, utsogoleri wamchigawo cha Bua uthandizira kuti anthu agwirizane bwino mzigawo za aphungu, m’ma boma, komanso pa chigawo chonse cha Bua.

Chisale wati anthu ambiri amene adzavote pa chisankho cha 2030 adzakhala achinyamata, choncho mkoyenera kuika patsogolo achinyamata pa nkhani za utsogoleri.

Iye wanenanso kuti achinyamata sayenera kusankhidwa chifukwa cha zaka zokha, koma ayenera kukhala anthu a khalidwe labwino komanso omwe ali ndi luso la utsogoleri.

Apa Chisale wapempha mamembala a MCP kuti amupatse mwayi wotsogolera chigawo cha Bua, ponena kuti ali wokonzeka kugwira ntchito m’ma Constituency ndi maboma onse omwe ali mchigawochi.

Wolemba: Ben Bongololo

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading