
Ena mwa ogwira ntchito m’boma ku Kasungu anauza Phungu wawo Ken Kandodo kuti akameme aphungu amzake kuti boma liwakwezere malipiro.
Poyankhula pa mkumano omwe a Kandodo anachititsa ndi anthuwo, m’modzi mwa anthu ogwira ntchito m’boma anati;
“Pitani ndithu mukawanong’oneze kuti malipo aonjezere ndi 44%, paja olira samutseka pakamwa, komanso sachita kumupangira. Pajatu tilipo 300,000 ndipo awa ndi mavoti ambiri ngati mukufuna kuti boma likhale lomweri,” anatero mphunzitsi wina kuuza a Kandodo.
Iye adauzanso a Kandodo kuti kuwonjezera malipiro kufika pa 44% kungathandizile kutukula maphunziro ponena kuti zimakhala zovuta kuti aphunzitsi agwile ntchito yawo modzipereka kaamba kakuti ambiri amayika chidwi chawo kugwira maganyu ndi cholinga choti apeze kangachepe.
Masiku apitawa ogwira ntchito m’boma anachita zionetsero pofuna kupempha boma kuti likweze malipiro awo koma zionetserozi zinasokonekera pamene anthu ena adayamba kuchita chiwembu anthu amene amachita zionetserozi.