Chitetezo sichilibwino ku Nyumba ya Malamulo

Advertisement
Parliament

Dzulo anthu ena omwe akuganizilidwa kuti ndi a Malawi Congress Party (MCP) anabowola mateyala a galimoto za a Phungu achipani cha Democratic Progressive (DPP).

Lero mu nyumbayi aphungu a chipani cha DPP adandaula kuti chitetezo chawo chili pachiwopsezo pa zomwe zinachitika dzulo.

A Victor Musowa phungu wa dera la Mulanje Bale ati, anthu omwe anavala makaka a chipani cha MCP ndi ena mwa anthu omwe awonedwa pa ma camera achinsinsi omwe anayikidwa m’nyumbayi.

Musowa wati anthuwa anapita pa galimoto ya m’modzi mwa aphungu a chipani cha DPP ndikupanga chiwembu chophwetsa mateyala. Izi zimachitika a chitetezo ena a kunyumbayi akuwonelera.