Sindingapangire kampeni UTM itandipatsa mavoti 21 okha – delegate wa chipongwe wabangulitsa Kaliati

Advertisement
Patricia Kalitati

Yemwe anali mlembi wa chipani cha UTM komaso ponda apa nane mpondepo wa malemu Saulos Chilima, Patricia Kaliati, watemetsa nkhwangwa pamwala kuti sangapangile kampeni chipanichi pomwe adapeza mavoti 21 okha ku konveshoni yapitayi. Iye waloza chala Chilima pakulephera kwake.

Malingana ndi kilipi (audio clip) yomwe anthu akugawana m’masamba a mchezo momwe amacheza ndi anthu ena, “Akweni” ati sangachite chibwana chanchombo lende chomema anthu kuti adzavotele chipani cha UTM pa zisankho zikubwerazani pomwe awonetsedwa za kuda ku konveshoni yapitayi.

“Pa ma voti 748 sangatenge 21 kumpatsa Patricia Kaliati nde muyembekezera ineyo kubwera kuzachita kampeni ya chipani cha UTM, pokhapokhatu bambo anga atadzuka kwakufako ndikapeze ali pampando pankhonde kunyumba kwanga apopo nde nditha kupangadi izozo koma popanda bambo anga kudzuka ine singachite zibwana zopangira kampeni UTM, over my dead body,” wabangula Kaliati kwinaku abambo ndi amayi ena akuyipatsa moto chapansi pansi.”

Kaliati anapitiliza ndikuloza chala malemu Chilima yemwe anali mtsogoleri wa chipanichi ponena kuti ndi yemwe adapangitsa kuti iye apezeka mavoti ochepa chonchi.

“Mwinaso mavoti 21 wandipatsa ndi Saulos-yo ndipo iye analolelanji kuti izi zichitike, ine ndivutike chifukwa cha legacy ya chilima? Sindingachite zimenezo,” watelo Kaliati. “Nde wina akamati Kaliati sangapange chiganizo chifukwa cha SKC, kodi SKC ali moyo? Anakakhala moyo bolatu bwezi tikuti tizichita manyazi koma sali moyo.”

Kaliati yemwe akuti wakhala akudutsa muzowawa chifukwa cha chipani cha UTM, wanenetsa kuti apanga chiganizo chomwe wati chikhala chabwino. M’kukambilana kwake ndi anthuwa mu kilipiyi, Kaliati amayeza ziganizo zosamukira ku zipani za MCP, AFORD, UDF komaso DPP.

A bambo omwe amayankhula nawowo anamuuza Kaliati kuti afufute maganizo opita ku chipani cha MCP ponena kuti chilibe tsogolo ndipo pakutha pa miyezi khumi ikudzayi chipanichi chikhala chikutuluka m’boma nde adzasowa kolowera.

Advertisement