
Timu ya FCB Nyasa Big Bullets yagonjetsa timu ya Creck Sporting 4-1 kutola ma points onse atatu lero m’masewelo a mu 2025 TNM Super League omwe anachitikira pa bwalo la Kamuzu mu mzinda wa Blantyre.
Zigoli ziwiri mchigawo choyamba kuchokera kwa Wongani Lungu pa mphindi ya chi 19 ndi Babatunde Adepoju pa mphindi ya 40 zinali zokwana kutseka gawo loyamba la masewelowa (2-0).
Mponda anadalira Innocent Nyasulu pagolo, Mologeni, Joseph, Mpokera, Mkwate,Salima, Singo Babatunde, Lungu, Jovinala ndi Lloyd Àaron , pomwe mphunzitsi Joseph Kamwendo anayambitsa Brighton Munthali pagolo, Hadji Wali, Aaron, Ademola, Talandira, Bayo, Hardy, Kondwani, George, Patrick ndi Peter.
Mgawo lachiwiri pa Mphindi ya 52 Chikumbutso Salima anamaliza mpira omwe analandira kuchokera kwa Wongani Lungu kuzisiya zinthu pa 3-0.
Patangotha mphindi zitatu anabwera Yamikani Mologeni kudzawonjezera chipongwe mpira omwe analandira mosinthana kuchoka kwa Chikumbutso Salima 4-0.
Anyamata a Kamwendo anapeza mpata ndi kumuthidzimula Innocent Nyasulu chimodzi kuti asachoke ndi mbiri yoyera, chigoli cha Kondwani Chilembwe pa 90 (4-1).
Mphunzitsi wa Creck Joseph Kamwendo wati anakanika kupeza mpata kuti akhonza kugoletsa, ndipo anyamata ake sanasewere m’mene amayenelera kuchitira.
Iye anati anapeleka ulemu ochuluka, ndipo avomeleza kugonja kwawo ponena kuti league yangoyamba kumene.
Mphunzitsi wa FCB Nyasa Big Bullets Peter Mponda wati ndi okhutira ndi zigoli zomwe apeza ndipo nkhawa ndi yogoletsetsa chigoli chawo nthawi yokutha kale.
Iye wati anyamata ake achita zonse zomwe anakambirana, ndipo wati masewelawa pokhala achiwiri ntchito idakali.
Bullets yapambana masewela ake achiwiri mu league yayikulu, ndipo ili pamwamba ndi ma point 6 chifukwa cha kuchuluka kwa zigoli Komanso chifukwa sinachinyitse zigoli zambiri pomwe Creck yasenza ma timu onse pa mndandanda.