A Navicha adzudzula ndondomeko yolembetsela voti

Advertisement

Mtsogoleri wa mbali yotsutsa boma wa DPP kunja kwa nyumba ya malamulo a Mary Navicha, ati atengela ku nyumba ya malamulo nkhani yokhudza kalembela wa voti kuti akawunikenso lamulo logwiritsa ntchito chiphaso cha unzika poponya voti kuti zichotsedwe.

Polankhula mu msonkhano wa olemba nkhani ku Golden Peakock mu mzinda wa Lilongwe, a Navicha ati apempha bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) kuti adzalole anthu onse amene ali ndi ziphaso komanso omwe alibe kuti adzalembetse mu kawundula wa voti yemwe ayambe mwezi wa Sepitembala kukonzekera chisankho cha atsogoleri chaka cha mawa.

A Navicha ati ganizoli ladza pamene chipani chawo cha Democratic Progressive (DPP) chaona kuti kulephera kwa bungwe lowona zakalembela wa nzika kulemba anthu komanso kutulutsa ziphatso m’madela ambiri makamaka ku chigawo cha kum’mwera kumene anthu ochuluka sanalembetse kukuyika pa chiopsezo ndondomeko ya mavoti.

Ena mwa omwe analipo pa msonkhanowu ndi a George Chaponda, mlembi wa chipanichi a Clement Mwale, a Jappie Mhango ndi Mary Mpanga mwa ena.

Boma la Malawi linayamba kugwiritsa ntchito chiphaso cha mzika polembetsa kuti munthu athe kuponya voti yosankha khansala, phungu komanso mtsogoleri wa dziko mu chisankho cha patatu cha mchaka cha 2019.

Advertisement