Makhansala ku Zomba akufuna kuchotsa khansala nzawo pa udindo

Advertisement

Makhansala ena amu Mzinda wa Zomba komanso Phungu wamu mzindawu Bester Awali adakonza upo wofuna kuchotsa Khansala Rams Kajosolo pa udindo wa wapampando wa Komiti ya ntchito zachitukuko.

Kudzela muchikalata chawo chomwe adalemba ndipo chidasayinidiwa ndi Phungu wamdera lapakati mu Mdzinda wa Zomba Bester Awali, komanso makhansala ena Christopher Jana ndi Edah Mkula ndipo chidawerengedwa munsonkhano wa Full Council omwe udachitika Lachisanu, Iwo ay wapampandoyo akulephera kugwira bwino ntchito yake ndipo akulephera kuyendera mapulojekiti omwe akugwiridwa munzindawo.

Koma poyankhapo zomwe zidalembedwa muchikalatacho, yemwe akugwiridzira udindo wa Mkulu wa Mzinda wa Zomba (Chief Executive Officer) yemwenso ndi Mkulu woona za Mapulani ndi Chitukuko a Fred Nankuyu adati zomwe zidalembedwa muchikalatacho ndi zopanda pake ndipo zilibe mfundo zeni zeni zogwira mtima.. Iwo adati malamulo oyendetsera maboma ang’ono (Local Government Act) amafotokodza kuti Khansala akasankhidwa mu Committee iliyonse palibe amene angamuchotse pawudindowo mpaka nthawi yake yokhalira pawudindowo itatha.

Pamenepa a Nankuyu adadzudzulu omwe adalemba chikalatacho kuti izi akuchita chifukwa cha zandale komanso kaduka choncho adagamula kuti Khansala Kajosolo apitilidabe kugwira ntchito yake ngati wapampando wa komitiyo.

“Malamulo oyendetsera maboma ang’ono mulibe lamulo lomwe limafotokodza kuti Khansala akasankhidwa pa udindo mu komiti iliyonse akhoza kuchotsedwa ndi anzake ngati sakugwira ntchito bwino ndiponso muchikalata chanuchi mulibe mfundo zogwira mtima zomwe tikhodza kumvomeredza kuti Khansala Kajosolo achotsedwe ngati wapampando wa committee ya works.” Adatero a Nankuyu.

Khansala Christopher Jana, Edah Mkula komanso Phungu wamdera lapakati mu Mdzinda wa Zomba Bester Awali onsewa ndi achipani cha DPP ndipo Khansala Rams Kajosolo ndi wachipani cha PP.

Follow us on Twitter:

Advertisement