Bwalo lalikulu la Zomba lalamula kuti ana osunga madiledi aziwalola m’masukulu a boma

Advertisement

Bwalo lalikulu ku Zomba lagamula kuti Unduna wa za Maphunziro kuti uzilola ana osunga madiledi m’masukulu a boma.

Popereka chigamulocho, Judge waku High Court ku Zomba Justice Patrick Chirwa yemwe amapereka m’malo mwa Justice Zione Ntaba adati kuletsa ana a ma rasta kuphunzira ndikuwaphwanyira ufulu wawo wamaphunziro.

Iye adati ofesi ya mlangizi wamkulu wa boma pa malamulo ndi ofesi ya boma choncho iyenera kumagwira ntchito yake motsatira malamulo komanso isamangotetedza zinthu zolakwika.

Justice Chirwa adatinso unduna wazamaphunziro uchotse lamulo lomwe limaletsa ana ama rasta kumaphunzira ali ndimadiledi ndipo udziwitse sukulu zonse mdziko muno zakuchotsedwa kwalamuloli pofika pa 30 June.

Pamenepa Justice Chirwa adalamula ofesi ya mlangizi wamkulu wa boma kuti ilipire ndalama zonse zomwe zawonongedwa pamulanduwu.

Poyankhulapo, loya yemwe amayimilira ma Rasta pamulanduwu Chikondi Chijozi adati ndiwokhutitsidwa ndi momwe chigamulo chaperekedwera.

Chijozi adati akukhulupilira kuti mbali ya Boma itsatira chigamulocho popeza kunyozera chigamulo cha khoti ndi mulandu waukulu. Pamenepa iye wati mulanduwu ngakhale watenga nthawi kuyambira chaka cha 2020 iwo asangalala kuti tsopano wafika kumapeto.

Poyankhulapo, m’modzi mwama Rasta Reuben Chapunga Chilembwe adati chigamulochi chawasangalatsa chifukwa ana awo adzipita ku sukulu za Boma popanda vuto.

Omwe anadandaula ndi Rasta Ali Nansolo pamodzi ndi Rasta Mahala Mbewe omwe ana awo adakanidwa kukayamba school ku Malindi Secondary School ku Zomba ndiku Blantyre Girls Primary School.

Follow us on Twitter:

Advertisement