Bwalo la milandu lakana kupereka belo kwa Sing’anga


Bwalo la milandu ku Zomba lakana kutulutsa pa bail sing’anga Malizani Pawoneke Salizeni yemwe akumuganizira kuti anagwiririra ana achitsikana anai osakwana zaka 17 zakubadwa.

Woweruza Martin Chipofya wati mlandu omwe adapalamula sing’angayu ndiwaukulu ndipo ndikosayenera kupereka belo ndipo bwaloli layamba layimitsa mulanduwu mpaka pa 8 May nthawi ya 10 koloko mamawa.

Sing’anga Malizani Pawoneke Salizeni yemwe alindi zaka 23 zakubadwa adapalamula mulanduwu m’mudzi mwa Diamond mdera la Sub T/A Ntholowa Boma la Zomba.

Pakalipano  Malizani Pawoneke Salizeni akumusunga ku Ndende yayikulu ya Zomba.

Follow us on Twitter: