Ambuye akukanthani nonse onyoza a Chakwera – watero Manganya


A nduna oona za chikhalidwe a Michael Usi amene amadziwikanso ngati Manganya ati Mulungu achita ndi a Malawi onse onyoza a Chakwera.

Polankhula pa mwambo okumbukira M’busa John Chilembwe ku Chiradzulu, a Usi anadzudzula a Malawi amene ntchito yawo imakhala kudzudzula atsogoleri.

Mukuona kwawo bambo Usi, amenenso ali mtsogoleri wachiwiri wa chipani cha UTM, a Chakwera pamodzi ndi achiwiri awo a Chilima akugwira ntchito yotamandika yofuna kusintha a Malawi. Koma ati pamene anthuwa akukangalika chonchi, a Malawi ena sakukondwa iyayi.

Kulingana ndi kufotokoza kwawo bambo Usi, iwo ati a Malawi osakondwawa akhala akunyoza atsogoleri awiriwa mosalabadira kuzipereka kwawo. Pa chifukwa ichi iwo anachenjeza kuti Mulungu akantha anthu osayamikawa.

“Anthu onyoza atsogoleri, Ambuye akukanthani,” anatsimikiza a Usi.

Koma a Malawi ena adabwa ndi kulankhula kwa bambo Usi amene anatchuka ndi za nthabwala kudzera mu sewero la Tikuferanji.

“Kodi awa amaoneka ngati a nzeru chabe koma palibe chiripo kuteleku?” adabwa choncho athu ena pa masamba a mchezo.

Tipezeni ku Twitter