Asilikali awapempha akhale osunga khalidwe pomwe akupita ku DRC


Asilikali a Malawi Defence Force (MDF) awapempha kuti akhale osunga khalidwe komanso olimbikira ntchito yawo pomwe akupita kukasungitsa bata mdziko la Democratic Republic of Congo DRC mwezi wa January chaka chamawa.

Wayankhula izi ndi Chief of Staff ku Malawi Deforce Force, Major General George Jaffu Jnr ku Chikala Forest m’boma la Machinga pamwambo wotsekera maphunziro ankhondo wokonzekera kupita mdziko la DRC kukatsungitsa bata ndi mtendere kwa anthu amdzikolo.

Major General Jaffu Jnr wati msilikali ayenera kukhala osunga mwambo komanso wokhulupilika pofuna kupititsa patsogolo mbiri yabwino ya asilikali adziko lino.

Pamenepa iye wachenjeza kuti msilikari aliyense yemwe akakhale osasunga mwambo panthawi yomwe akugwira ntchito yosungitsa bata mdziko la DRC adzamubwedza kuno kumudzi ndipo ayembekezere kuti akadzafika kuno adzamupatsa chilango.

Mmodzi mwa akuluakulu asilikali ankhondoyu, wati asilikali a dziko lino ndiwokonzeka kukasungitsa bata ndi mtendere kwa nzika za dziko la DRC ndipo adati alindichikhulupiliro kuti asilikaliwa akagwira ntchito yotamandika panthawi yonse yomwe akakhale kumeneko.

Iye wati chiyambireni kutumidza asilikali adziko lino kukagwira ntchito yosungitsa bata mdziko la Democratic Republic of Congo chaka cha 2013, amsilikari adziko lino akhala akuchita bwino pogwira ntchito yawo mwaluso ndiponso molimbikira.

“Panthawi yomwe mukupita ku DRC musakayiwale kusunga mbiri yabwino yadziko la Malawi ndipo ndikupempheni kuti mukawonetse khalidwe labwino komanso musakayiwale kuti mwasiya mabanja anu kumudzi,” adatero Major General Jaffu Jnr.

Mu mau ake, Kazembe wadziko la United States of America kuno ku Malawi David Young wati ndiwokhutitsidwa ndimomwe wawonera asilikari adziko lino akukozekera maphunziro awo ankhondo ku Chikala Forest.

Ambassador Young wati amapereka ulemu kwa asilikali adziko la Malawi chifukwa chogwira ntchito molimbika komanso chambiri yawo yabwino panthawi yomwe akhala akuteteza miyoyo ya anthu komanso kuteteza ufulu wachibadwidwe kwa anthu adziko la DRC.

Pamenepa iye walangidza asilikali adziko lino kuti akapitilize kugwira ntchito molimbika panthawi yomwe akupita dziko la DRC. Iye walonjedza kuti dziko la America lipitiliza kuphunzitsa amtsilikari adziko la Malawi panthawi yomwe akukonzekera kupita kukasungitsa bata mdziko la DRC.

Poyankhulanso pamwambowo, kazembe wa dziko la Britain kuno ku Malawi David Pert wati asilikali adziko la Malawi ali ndi mbiri yabwino komanso wayamikira akulu akulu asilikali omwe amawayang’anira asilikariwa chifukwa choti akukwaniritsa zokhumba zawo.

British High Commissioner’s Pert wati asilikali adziko la Britain akhala akuphunzitsa asilikali adziko lino kwa masabata khumi ndipo walonjeza kuti dziko lake lipitiliza kuthandiza asilikali adziko lino chifukwa asilikaliwa ali mbali imodzi ya asilikali osungitsa bata a UN Peace Keeping Mission

Asilikali okwanira 731 a Malawi Battalion ndiwomwe akhale akupita dziko la DRC mwezi wa January chaka chamawa kukagwira ntchito yosungitsa bata ndi mtendere ndipo aka kakhala ka number 14 chiyambireni dziko la Malawi kutumidza asilikali mdziko la DRC.