Marinica wachenjeza a Malawi kuti asayembekezere zambiri ku COSAFA

Advertisement

Mphunzitsi wa Flames Mario Marinica wachenjeza a Malawi okonda mpira kuti asakhale ndi chiyembekezo chachikulu pomwe Flames ikhale ikukapikisana nawo mu mpikisano wa COSAFA wa chaka chino komwe ili mu gulu limodzi ndi Lesotho, Mauritius komanso Eswatini.

Timu yomwe ikhale pamwamba mu gululi izakumana ndi Senegal yomwe ibwere ngati alendo ku mpikisanowu mu ndime ya matimu asanu ndi atatu.

Ambiri mwa a Malawi okonda mpira mdziko muno ali ndi chiyembekezo chachikulu chifukwa akuona ngati matimu omwe Flames yaikidwa nao mu gululi ndi ophweka kuwagonjetsa, koma mphunzitsi wa team ya dziko lino Marinica wachenjeza kuti pali zambiri zofunika kukonza kuti team yi ichite bwino ndipo pakufunika osayembekezera kwambiri zotsatira zosangalatsa kuchokera ku mpikisanowu.

Koma mphunzitsiyu walimbikitsa anthu kuti akhale ndi chikhulupiriro komanso ogwirana manja chifukwa chilichonse ndichotheka ndipo timu iliyonse imene imalowa mu mpikisano ngati umenewu imakhala ndi mtima ofuna kupambana.

Mpikisano wa COSAFA ukuyembekezera kuyamba pa 5 ndipo uzatha pa 17 July 2022 mu dziko la South Africa.

Malingana ndi mndandanda wa COSAFA, pakali pano South Africa ili pamwamba pa ma timu ochita bwino, kenako Zimbabwe, Mozambique, Malawi, Namibia, Comoros, Botswana, Lesotho, Eswatini, Madagascar, Seychells, ndipo kumapeto kuli Zambia.

 

Follow us on Twitter:

Advertisement