Mvula iyamba lachisanu, atero a zanyengo

Advertisement
Storm

Nthambi yowona zanyengo ndi kusintha kwa chilengwedwe yati mvula iyamba kugwa mdziko muno lachisanu sabata lino.

A Jolam Nkhokwe omwe ndi mkulu wa nthambiyi ndi omwe anena izi polankhula ndi wailesi ina mdziko muno.

Malingana ndi a Nkhokwe, mvula ikayamba lachisanu ipitirira kugwa mpaka lamulungu.

Padakali pano, pali nkhawa chifukwa nyengo ya mvula yachedwa kuyamba ndipo kutentha komwe kunayamba mu Okotobala kudakapitilira.

Mu madera ena alimi anadzala kale mbewu ndipo akatswiri a zaulimi ati alimiwa adzalenso mbewu ina.

 

Advertisement