Kutentha kupitilira sabata lino, atero a zanyengo


Unduna wa zachilengedwe kudzera mu nthambi yake yowona zanyengo yati kukhala kukutentha mzigawo zonse za dziko lino kuyambila lolemba kufikira lachinayi lino kaamba ka mphepo yotchedwa Mvuma yomwe yikhale yikuwomba pa nyanja ya Malawi.

Kudzera mkalata yomwe nthambiyi yatulutsa yati, anthu akhale tcheru kuyambira la chisanu mpaka lamulungu mzigawo zonse kamba kakuti mvula yamkuntho yizakhala kuti yayamba kugwa yomwe yidzabwere ndi chiphaliwari.

“Mwezi uno wa December kukhala ziphaliwari ndipo tikupempha anthu kuti nthawi zonse akawona ziphaliwali zayambapo azithawira mnyumba kuwopa kuwombedwa ndi mphedzi komanso zinthu zina zowuluka ndi mphepo,” iwo anatero.

Iwo apitilizanso kupempha ma khonsolo ndi nthambi yowona misewu kuti akonze ngalande kuti madzi asamasefukile.

Mtolankhani olemba nkhani zachilengedwe ku wailesi ya ku Dowa yotchedwa Yetu, Abraham Bisayi, wati mu nthawi ngati iyi anthu  ayenera kumatsatira mwachidwi nkhani za nyengo tsiku ndi tsiku komanso kumafufuza azibale awo momwe aliri kamba ngozi zimachuluka mu nthawiyi.