Boma lati lichotsa eni migodi m’malo okwelera minibasi

Advertisement

Eni minibus atadandaula kuti akumapereka ndalama zambiri kwa eni migodi komanso oitanira, boma lati lichotsa anthuwa m’malo okwelera minibasi.

Nduna ya Zofalitsa Nkhani, yemwenso ndi m’meneri wa boma a Gospel Kazako ndi omwe anena izi m’mawa wa lero pa msokhano wa atolankhani Blantyre.

Malingana ndi a Kazako, kuyitanila ma minibus kwathetsetdwa komanso zoti ena ndi eni migodi m’malo okwelera minibus zatha chifukwa m’malamulo a dziko la Malawi mulibe zimenezi.

A Kazako ati anthu ojiya ndi omwe amadzitcha eni migodi mu malo okwelera basi achoke mu malowa.

A Kazako ati apolisi ndi nthambi zina zonse zokhudzidwa awadziwitsa kale.

Sabata latha, eni minibus, a Minibus Owners Association anadandaula za ganizo la boma loti iwo adzipereka K3400 pa nthawi iliyonse yomwe minibus ikudutsa pa zipata zomwe boma lamanga monga pa Chingeni Toll Plaza.

Iwo anati amapereka kale ndalama kwa ojiya omwe amaitanira anthu kukwera minibus komanso eni migodi pa malo okwerera minibasi.

A MOAM anachenjeza kuti mawa ma minibasi awo sayenda ngati boma silimva madandaulo awo.

Polankulapo padandaulo la za ndalama zopereka pa chipata, a Kazako ati boma silitsitsa mtengo womwe linakhazikitsa.

Iwo ati ndalama zomwe zizitoledwa kwa odutsa pa chipatachi ndi zokonzera misewu komanso kumangira ina.

Advertisement