Mitsutso yathandiza kuthetsa ziwawa – NICE


Bungwe la National Initiative for Civic Education (NICE) ku Mulanje lati mitsutso yomwe bungwelo mogwirizana ndi bungwe loyendetsa za zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) yathandiza kuchepetsa mikangano yomwe idalipo m’mbuyomo m’madera momwe anthu akupikisana pa maudindo a khansala komanso phungu m’nyumba ya malamulo.

Izi alankhula ndi wapampando wa Advisory Forum ya NICE Smart Maruwasa m’mdera la pakati ku Mulanje pa Ulongwe pomwe padali mtsutso wotsiriza mbomali lachiwiri.

Maruwasa: Mitsutso yathandiza

“Ku Mulanje kuno kunali milandu yosiyanasiyana yokhuzana ndi zisankho. Koma pamene tinayambapo mitsutsoyi, paoneka kuno kusintha kulipo ndipo ndikadakondwa mtendere umene wabwera kamba ka mitsutso imeneyi upitilire kufikira tsiku loponya chisankho pa 21 May, 2019,” adatero a Maruwasa.

Polankhulapo, wachiwiri kwa wamkulu wa polisi mbomali adachenjeza anthu za ziwawa pa nthawi yokopa anthuyi nawatsimikidzira kuti iwo ngati apolisi sazalekerera ziwawa koma kumanga onse oyambitsa.

Mu boma la Mulanje muli madera asanu ndi anayi ndipo mitsutso yachitika mmadera monsemo.

Wolemba: Phillip Banda, Mtolankhani wa MEC