Khansala wa MCP asankhidwaso kukhala wapampando wa nkhonsolo ya Salima

Advertisement
Salima

Pamene kwangotsala miyezi yowelengeka kuti a Malawi aponye voti, Khonsolo ya Salima yasankhaso a Everson Mpayani kukhala wapampando wa bomali mu chisankho chomwe chinachitika lolemba m’maofesi a bomali.

A Mpayani omwe analinso wapampando mu zaka ziwiri zapitazi ndiwochokera ku chipani cha Malawi Congress Party (MCP) awina ndi mavoti 10 zomwe zikusonyeza kuti apitilira kutsogolera khonsoloyi mpaka mu chaka cha 2019.

M’mau awo iwo anati kupambana kwawo kwasonyeza kuti amagwira bwino ntchito ndi makhansala anzawo komanso aphungu posatengera zipani zomwe amachokera.

Salima
Mpayani (ayimlirawo) kulankhula atangosankhidwa kukhala wapampando pa nkumano wa khonsolo ya Salima

“Ine ndiri okondwa kuti makhansala anzanga komanso aphungu omwe ndimagwira nao ntchito andikhulupilira pondisankhanso kuti ndikamalizitse ntchito yomwe ndinaiyambapo mzaka zapitazo,” anatero a Mpayani.

Pa nkumano omwewu zadziwikanso kuti boma lakonza ndondomeko zatsopano zomwe mafumu adzilandira malipiro awo kudzera ku banki ndi cholinga chofuna kuchepetsa kusakazidwa kwa chuma cha boma.

Bwanankubwa wa khonsoloyi a Charles Mwawembe anauza msonkhanowu kuti izi zichepetsa vuto lomwe chuma cha boma chimasakazidwa kudzera mu ogwira ntchito a bodza.

Iwo anati khonsoloyi yagwilizana ndi bank ya NBS kuti idzathandiza mafumu ang’onoang’ono kutsegula ma akaunti powayendera m’madera ao.

Advertisement