Osamangolubwalubwa, CAF si za ana

Advertisement
Be Forward Wanderers

Manoma ametedwa mpala likuwala ku DR Congo pamene anzawo a Masters Security nawo angoti mwachaje satafuna, kubwela chimanjamanja ku Angola.

Matimu onse awiri amene anakaimila dziko lino ku mpikisano wa CAF abwela chimanjamanja, osaona golo olo kamodzi.

Anayamba kuonetsedwa zowawa anali anyamata a Masters Security pachiwelu. Pa masewelo amene anachitika mu dziko la Angola, timu ya Masters Security inaswedwa mosayang’ana nkhope.

Be Forward Wanderers
Manoma ametedwa mpala.

Zigoli zisanu ndizo zinaphamikidwa kwa timu ya Masters powadziwitsa kuti CAF si ya ana ongolubwalubwa.

Pa zisanu zonse zimene iwo analandila, anyamata a Masters sanabwenzemo olo chimodzi.

Dzulo lawisili ndiye linali la nyerere, aja anapitila ku CAF mantha a chindapusa aja.

Nyerere zinapita ku DR Congo kumene sanachita kukumbutsidwa kuti mpira si phada ndipo katswili wa ligi ya ku Malawi, kwa anzathu uku atha chabe kukhala bolera.

AS Vita, timu imene yajompha nyerere dzulo inaswa makofi akatswiri a ku Malawi kuno awa kanayi. Mopanda chisoni konse olo nthumadzi.

Nyerere sizinaone ndi komwe golo la anzawo.

Advertisement

3 Comments

  1. Pepani bola mwakaonako kwawo kwa yondo sister,kapena Dr sakis

  2. koma amwene ndinu aja amati abullets mumalemba nkhani mumchichewa aja eti?? mwadziwika tsopano.tsopano dziwa ichi…..noma ndiakatundu ndithu ndipo olo udzainyoze chotani siidzasintha….ndiposo ndisakunyengelele..panyapako..

Comments are closed.