Wapolisi amangidwa chifukwa choyaka kunyumba ya Obama

Advertisement
Malawi

Inatchuka nkhani yoti Wapolisi wa zachitetezo ananjatwa kamba kopita ku chimbudzi ku nyumba ya nduna zoona zophunzitsa anthu.

Malinga ndi malipoti amene amagawidwa mma Facebook ndi WhatsApp, ati Wapolisi amene amapeleka chitetezo ku nyumba ya Mayi Grace Obama Chiumia anamva m’mimba kutentha. Ati atamva m’mimba kutentha, anaganiza zokapambuka osadziwitsa abwana ake a Obama.

MalawiAti abwanawo atabwela ndi kupeza kuti iye akutuluka ku chimbudzi chawo, basi analamula kuti wapolisiyo amangidwe.

Koma polankhulapo pa nkhaniyi, Apolisi ati ndi zabodza zoti wapolisi anamangidwa ku nyumba ya a nduna anamangidwa chifukwa chopita ku chimbudzi.

Mneneri wa Apolisi chigawo chapakati a Nolletie Chimala anauza Malawi24 kuti ndi zoona zoti wapolisi ananjatidwa kunyumba ya a Chiumia.

“Koma sichinali chifukwa choti anapita ku chimbudzi,” anatelo a Chimala.

Iwo ati wapolisiyu amene anatumidwa kuti akapeleke chitetezo kunyumba kwa a Chiumia, analedzera ali pa ntchito. Apolisi atazindikila izi anakamunjata ndi kutumiza wapolisi wina.

 

Advertisement

30 Comments

  1. how can we believe its not just story-twisting, the first-hand info was the gate was unmanned coz the gateman went to answer the call of nature at the minister’s toilet, anow this time he was drunk… #God_is_watching

  2. Ulonda ndi sober zizimagwilizana umafuna uziionela patali nanga kunabedwa ngati? aaa ukafuse mulonda wa G4s akuuza kuti amangoyendela bola guit and nomal stuasion basi

  3. Moti uyaka aunenako , ndiye kuti aunena zoledzela? Zinazi zimalankhulidwa koma apapa ndimaitenga nkhaniyi ngati Kuala Kwa moto

  4. Chimbudzi chabwanawo amalowamo wokha basi? Nanga alonda alibe chawo?

  5. Kodi Kunyela Ndi Mulanduso? Kunya Saletsa Koma Manyeledwe.Inunso A Malawi Twete Foru Muzilemba Zinthu Zomveka Osalemba Nga Ma Sekeretare A Banki Nkhonde…Iyaaa!

  6. Kodi inu a Malawi 24 mukati kuyaka mukuthandaudza chiani? Mudzitiudza chichewa cholondola not kuyaka. Mukanati adamwa mowa ndipo adalezera

  7. hahahahaha crazy country with inconsistent and stupid leaders, really mpaka arresting him? Thats a professional issue the guy was negligent he deserves some disciplinary measures…..if this is the case then peter deserves life sentence he has been sleeping on duty all along

Comments are closed.