Chuma chikuyenda bwino, onani galimoto zonsezi – Mutharika

Advertisement
Mutharika

Ngakhale Atoti Manje anadandaula kuti pa galimoto zonse zili mdziko muno palibepo olo imodzi ya m’bale wawo, Mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika wati a Malawi moyo wawo ukuyenda bwino kamba koti mu dziko muno mukulowa galimoto zochuluka.

Mu uthenga wawo wa chaka cha tsopano, a Mutharika anati chuma cha dziko lino chinaphukila mu chaka cha 2017 ndipo chinkilakila kukwela.

Muthariaka: Chuma cha dziko lino chinaphukila mu chaka cha 2017.

“Kutukuka sikophweka iyayi, zimafunika kuleza mtima. Pang’ono pang’ono tifika pamene timafuna,” anatelo a Mutharika.

A Mutharika ananena kuti umboni oti zinthu zikuyenda ndi galimoto zambiri zikuyenda pamseu.

“Muli galimoto zambiri m’dziko muno, zambiri zalowanso chaka chomwe chapitachi. Ndikamayenda ndikuona galimoto zambiri zabwino. Tikutukuka,” anatelo a Mutharika.

A Mutharika anaonjezelapo kuti kubwela kwa galimoto zochuluka m’dziko muno kwabweletsa mwayi wa ntchito m’dziko muno maka kwa achinyamata.

“Chifukwa cha galimoto zambiri, kwabwela malo ambiri othila mafuta. Malo amenewa akulemba ntchito achinyamata ochuluka. Apa kuwathandiza kuti apeze ntchito,” anatelo a Mutharika.

A Mutharika anaonjezelapo kuti ngakhale ku midzi, anthu akusiya kuyenda pa njinga ya kapalasa ndipo ayamba kuyenda pa yamoto tsopano.

Iwo anaziyamikila kuti ngakhale anthu othandiza dziko lino analeka kulithandiza, koma iwo agwila dziko lino mpaka osapunthwa.

Advertisement

117 Comments

 1. Ambiri amene tikuyankhafe ndamene tilibe galimoto.Koma eni magalimoto ali phe.A President akuyerekeza ndi m’mbuyomo pamene magalimoto ankabwera ochepa mdziko muno.sakuti mavto muno mulibe ayi.DPP WOYEEEEE!P!!!?!!!!@&#*;%:??.;!!##**#!!!$_$@@*^_^*:-D:-P:-X:-X:-**^_^*-_-#-_-!:-|$&#**;!!!!!!!!

 2. vuto lawo loyamba ndilimenelo.Sakudziwabe kuti malawi muno munthu modzi amatha kukhala ndi galimoto 1000pamene wina akadalipidwabe ndalama yokwana 20000.ndalama yogulira galimoto aiba kuti.Mwina akatangale womwewo.

 3. Ine anga ndi matha basi ,anthu akumudzi akukhala movutika,kusowa zakudya inu abwana ndi kumati zinthu zili bwino.zoona zimenezo anthu akumwa madzi oipa inu abwana muli pheeeeeee,lero mukuti zili bwino.owo ngati abwana ananu akugula magalimoto dziwani kuti anthu ambiri akuvutika chifukwa cha inu abwana.kuba too much boma lanuli mr pitala

 4. Ine anga ndi matha basi ,anthu akumudzi akukhala movutika,kusowa zakudya inu abwana ndi kumati zinthu zili bwino.zoona zimenezo anthu akumwa madzi oipa inu abwana muli pheeeeeee,lero mukuti zili bwino.owo ngati abwana ananu akugula magalimoto dziwani kuti anthu ambiri akuvutika chifukwa cha inu abwana.kuba too much boma lanuli mr pitala

 5. Inenso ndi me anthu andare koma kunenena chirungamo kumalawi kuno kukusintha or miseu ikumag’ edwa yabwino yabwino kusiyana ndi mbuyomu and sizingachitike zosezi one time ai tiyeni tixithokodza ( guys) and mpano kwayamba kumangidwa ma mall ,shoprite ndizimene zili ma process and mwina ndikutheka kuti simuwerengako now’s Malawi muno

 6. Galimotozo ndi zako? Who the hell are you, to talk shit in front of poor people in the country? When boosting you mustn’t forget that nothing last forever mbudzi yamunthu inu, onsewa sangakhale opusa mkukhala ochenjera inuyo nthawi ikubwera muzatilipira izo nde mudziwe,

 7. Kodi apresident mutu mu amakumetani kodi amameta choncho ngati mkaziyo ndani munakadziwa kapena kuona zimanyasa bwanji ameneyo ndiamene amachosa nzeru zanu za u professor wanu bambo

 8. Anthu akugula magalimotowo ngati umaunza ndi iweyo ndinzeru nzao zimenezo alippo muthu unamuunza kuti apange chitukuko ndindani umuchulue dzina kuti dziko lidziwe ,koma chaponda munawaunza kabedwe kandalama kuti asangalala ndi Ana ake onsati Ife iwe ndiye nyani Monkeys

 9. Chuma cha president choka ndi chimene chikuyenda.azaona chaka cha mawa ayenera kuzampasa mazilo okha.muwera 0 makati 0 ndiponso kumpoto 0.achoke chotawa mmmmm

 10. I will never trust politicians chifukwa amalankhula mosalingalira zawo zikamayenda amaona ngati wina aliyense zake zikuyenda koma akanadziwa mmene amalawi tikuvutikiramo akanachepetsa kulankhula motumbwako

 11. I remember bro wake anatiso,,ngati kulibedi fuel mdziko muno pitani pamsewu tikaone ngati sakugundani kkkkkkk mutharika family

 12. Tiyeni Ku mudzi tikaone if people have the basic needs then we can say all is well. Mu town mwachuluka cash gate it won’t be the right litmus paper for good economy

 13. Zoti 2019 ikubwela ndipo tidzavota sakudziwa,ndipo amalawi tigwilane manja ameneyu ndie wotionjeza, mbavazokha ndizomwe zikunjoya mu bomalake losekelela umbava ndi umbanali.

 14. Galimoto? Magalimoto akeso makatoni aku Japaniwa? Koma akuluwa akudziwa mmene anthu akuzunzikira mmidzimu plus mma town ang’onoang’onomu? What about street kids ali mbwee mtowniwa? Ichi ndi chitsirudi eti?

 15. Ndianthu Angati akumudzi omwe agula magalimotowokodi pulezidenti sanganene kuti zinthu zikuyenda bwino kamba kowona anthu atown andalama kale ena mza cashgate mkumati chuma chikunda bwino aaa!kuu apite ku midziku ndipo adzapepesa mawu amenewa kumudzi uku kuli mavuto oopsa osati chibwa akunenacho atown ambiri zimawayendela ndikale mchifukwa chake odathawa ku mudzi kuja kapena akulamulira anthu atown okha pamene anthu mbeu abeledwa ndi K30-50 fodya amwayi$2 ndiye munthu wakumudzi angagule galimoto pamenepa tiyeninazoni 2019 mposachedwapa mwatilanga osatimasewera zikomo.

 16. iwe wachamba pasana pano,,,m’mene ukukwapulira/kuba custom mo,tazipanga ngt Ku Mozambik ndku Zimbabwe kumatchipa macustom,,kmaso usuye zomatilanda magalimoto paboda KT Malawi itukuke

 17. Atoti manjewo ndi amene tikufuna atalamulira dzikoli kamba ka masomphenya awo pa anthu osauka osati olemela amagalimoto anuwo

 18. Ine koma ndinayamba kumumvesesano munthuyu…pena amakhara zoti akuyankhura zanzeru koma vuto ndi malongosoledwe ake…1 day I quoted “dziko la Malawi ndi la fodya kwambiri, nde za fodya zomwe mukupangazo musasiye chifukwa zimabweretsa chitukuko mdziko muno” just imagine

 19. uchitslu,wa mun2 wophunzr,, if he prezdise the malawians sakanalankhula zopusazo ,kumamidzi alind magalimoto ndyangt?& thoz hu owns magalimoto anagula ndyeo ?b4 expressn ua speech u shud draft it,,, prezdent wa ntown …

 20. Iwe pitala iwe!!!!!! oh ndingalakwepo kod ukuwagawira naiwe ndalama zogula ma galimotowo? So umafuna kut anthu asiyule2 kugula ndikumaliza kugulitsa amene anali nawo kut udziwe kut anthu akuvutika? Palikundu shit;!!!!!;

 21. whether u want or nt bt u as our father malawi plz sometimez if u want 2 talk 2de public like dis plz first of o u suppose 2 think abt de pipo hu were poor at o so w as malawian pipo w masn’t look how number’s of cars w hve in dis country nop. Bt w need development from u father malawi das y w choose u 2b our reader ok so mukamalakhura muziyamba nkaye mwaganizira athu omwe amakhala mkumuzi omwe mpaka mpano sanayambepo kulota maloto ozagula galimoto coz 2much cars is nt a development wht pipo excepted 4rm u 2019 is nt far mchimenecho mudziwe. Long live malawi

 22. IN THE PAST KALIATI SAID NGATI MAFUTA KULIBE KAGONENE PANSEU TIONE NGATI SIKUGUNDANI NOW D WHOLE PRESIDENT TALKING TO THE WORLD KKKKKKKKKK MALAWI IN TOP 3 Ov The Poorest God Hav Mercy

  1. where did you do your reasech about malawi be on postion number 3 of the poorest in the world can you please do reasech again and see what position of malawi

 23. Uyende owone galimoto ukunena za China. Anthu akukwera galimoto osati za China komanso galimoto nzosala wauze anthu za yesu kumalawi tikuvutika kuposa maiko onse apansi chifukwa chainu azigoleri adyera amkhwizi mulandile yesu

 24. KUNKHALA NDI GALIMOTO SIKUTUKUKA KWA DZIKO KOMA KUKHALA NDI MA COMPANY AMBIRI NDIWO MAYAKHO ADZIKO chifukwa aliyese apeza zochita .sizamisala ukukukamba apazi

 25. Bvuto ndilakuti Malawi ali magawo awiri tsono poti apresident amakhala ku malawi (1) mpake kumayankhura zopusa ngati zimenezi Sinanga umphawi womwe akukumana nawo anthu ochuluka omwe amakhala ku malawi (2) iwo sakuwudziwa komano chobvetsa chisoni ndi chakuti malawi wa anthu ambiriyo ndi amene akunzuzika ndi umphawi komaso ndi yemweyo amene amawavotera ndiye poti pali mawu ena akuti (m’dya nyemba amayiwala koma mtaya makoko samayiwala)mudzawadziwa amalawi nthawi ikubvera bwana wanga mungoti pheeeeeeeeeeeeeeeeee

 26. Nkuluyu saganiza anangowona magalimoto ntown ali anthu Zikuyenda kkkkkk Prof uyu ndi wa China ndithu.

 27. but can a gratuate or a normal person be happY ,n sayn tht our life standards has been improved ,jst bcoz of incoming of cars to our country, do i look lik ,i own a car?, if u r grown old ,,don’t deceive us please!!!

 28. To him chitukuko ndi magalimoto,magalimotowo alinawo ndi anthu angati,Kapena mmene iwowo amayamba kulamulira anthu ku Malawi analibe magalimoto?

Comments are closed.