30 August 2016 Last updated at: 6:59 AM

Chaponda achoka chothawa ku Mulanje

chaponda george chased 1

Anthu aku Mulanje kuthamangisa galimoto yomwe anakwera a Chaponda.

Nduna ya zamalimidwe dzulo lolemba pa 29 August inaona mbonaona pomwe gulu la anthu mu boma la Mulanje linamulumila mano ndi kumupitikitsa mu bomalo.

Ndunayo, a George Chaponda, yemwenso ndi phungu wa nyumba ya malamulo wa mu dera lina mu boma lomweli la Mulanje anapita mu bomalo kukayendera ntchito ya Blantyre Water Board yofuna kupatutsa madzi kuchoka ku Phiri la Mulanje kuti anthu a ku Blantyre ndi madera ozungulira azipulumukilapo.

Chaponda, yemwe anthu ena akuti chipani cha DPP chikumulinganiza kuti azakhale President kuchoka kwa a Peter Mutharika, anapita ku deralo zitamveka kuti anthu ena a ku Mulanje akukana zoti achotse madzi mu Phiri lawo.

George-Chaponda

A Chaponda anayenda wa uyo-uyo.

Iye analimbitsana mtima ndi mlembi wamkulu wa mu unduna wa zamalimidwe, a Erica Maganga, pamodzi ndi phungu wa ku Mulanje Pasani, a Angie Kaliati, kuti akamveledwa akapita ku deralo.

Zodabwitsa zinali zoti anthu atamva kuti kukubwela akuluakuluwo, iwo anathamangila ndi kutseka mseu ndi miyala ndi mitengo kuti galimoto za wofowofo za akuluakulu abomawo zisadutse.

Atafika a Chaponda ndi anzawo anatutumuka anthu atawapitikitsa ndi kuwauza kuti ngati akufuna kupatutsa madzi mu Phiri lawo, ayambe kaye adzala mitengo mu phirilo komanso awapatutsile ena kuti iwo azimwa.

Zitafika povuta, galimoto za a Chaponda ndi anzawo zinatembenuka, kubanduka ulendo wa komwe anachokera.104 Comments On "Chaponda achoka chothawa ku Mulanje"