Eagles ikudziwa kale zaife — Akidu


Fundi Akidu- Malawi24

Mphunzitsi wa timu ya Ekhaya FC Fundi Akidu wati timu ya apolisi ya Standard Bank Blue Eagles ikubwera pa bwalo la Mpira ikudziwa kale kuti ikudzakumana ndi timu yabwimo.

Polankhula poyembekezera masewero a lero a mu FDH Bank Premiership msabata ya chi 18, Akidu wati timu yake yakonzeka mokwana ndipo sakulora kuchinyitsa zigoli.

Iye wavomereza kuti Eagles ikuchita bwino kale mu premiership koma masewero a mu otolera ma point ndi ovuta basi, ndipo uwu ndi mwayi wa timuyi kuti ichite bwino.

“Blue Eagles ikubwera ikudziwa kuti Ekhaya takonzeka ndipo sitikuchinyitsa zigoli, uwu ndi mwayi wathu kuti tipange chirichonse kuti masewerowa tichite bwino ndipo tichita bwino osakaika” Akidu anatero.

Mphunzitsiyu wati akukhulupirira kuti timu yake igwirana mokwana pakati pa osewera akale ndi atsopano, potengeranso mwayi oti masewero ambiri mgawo lachiwiri akhala a pakhomo.

M’mawu ake mphunzitsi wa Blue Eagles Deklerk Msakakuona wati ngakhale apeza ma point ochepa chiyambireni gawo lachiwiri, iye akuyembekezera kuchita bwino pamaso pa Ekhaya.

Msakakuwona wati momwe timu yake yakonzekerera komanso kusewerera akuyembekezera kuti osewera aliyense amene apatsidwe mpata agwira ntchito moyenera.

Eagles yomwe otchinga pagolo wake Precious masamba akuthamangitsa nawo akatswiri wa pa golo, ikulowa m’bwalo 3 koloko masanawa iri pa nambala 3 ndi ma point 34 kulekana chabe ma point awiri ndi Bullets yomwe ikutsogolera mndandanda, ndipo apolisiwa akhonza kuchotsa maule patsogolo ngati angagonjetse anyamata a ku Ng’ombe.

Ekhaya iri pa nambala 7 ndi ma point ake 22 mu masewero onse 17.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading