Pomwe kafukufuku wokhudza ngozi ya ndege akupitirira, mboni ina yati zomwe zinachitika kuti anthu ena okhudzidwa anapezeka alibe zovala zina, sizachilendo.
Wapolisi wofufuza Harry Mbewe wawuza komiti ya kafukufuku wa ndege kuti mphamvu ya ngozi ya ndege imatha kuvula komaso kung’amba zovala za anthu okhudzidwa.
Iwo mayankhula izi pomwe anafusidwa kuti afotokoze bwino pomwe zithuzi zina zangozi zimawonetsa okhudzidwa ena monga malemu Saulos Chilima alibe zovala zina.
Malingana ndi kafukufukuyu, malemu Chilima anapezeka alibe zovala zina monga nsapo ndi jekete koma adapezeka atagwira kolona m’manja mwawo.
Mbewe wati ngozi ya ndegeyi itachitika ku Chikangawa pa 10 June, 2024, iye anafufuza pa makina a internet kuti apeze zina mwa zinthu zomwe zimapangitsa kuti zovala za anthu zivuke pangozi ya ndege.
Iye wati anapeza kuti ndizotheka zovala za munthu kuvuka nthawi ya ngoziyi kaamba ka mphamvu ya gravitational mchingerezi.
“Nditafufuza pa Google ndinapeza kuti ndege ikagwa, mphepo komanso gravitational force zimatha kuvula anthu kapena kung’amba zovala zaokwera ndege,” adatero Mbewe.
Koma apa m’modzi mwa akuluakulu a komitiyi adawafusa a Mbewe kuti nanga zinatheka bwanji kuti a Chilima anapezeka atavulidwa mpaka nsapato, taye, komanso jekete yomwe anavala pomwe kolona anali ali m’manja.
Koma Mbewe anatsutsa ponena kuti Chilima sanapezeke atavulidwa taye.
“Inetu ndinapita komwe kunasungidwa thupi la malemu Chilima, ndipo a Chilima taye pakhosi inalipo komanso anali atavala wotchi,” adatsutsa Mbewe.
Apa m’modzi mwa akuluakulu a komitiyi adakumbutsa Mbewe kuti malingana ndi zinthuzi zomwe zinatuluka ngoziyi itachitika, malemu Chilima anavala tisheti, ndipo pakhosi panalibe taye.
“Mwina poti zinachitika kalekale nde pali zinthu zina sindingakumbukire bwinobwino,” uko kunali kuyankha kwa Mbewe.
Komitiyi ikupitirira kumva maumboni osiyanasiyana pomwe ikufuna kupesa chomwe chinachitika pa nthawi yangoziyi yomwe idapha malemu Chilima ndi anthu ena asanu ndi atatu.
home-