Anthu omwe akukudyerani a Kapondam’gaga akukulakwirani


Kapondamgaga- Malawi24

Akatswiri pa nkhani za ndale alangiza yemwe anali mkulu woyang’anira anthu ogwira ntchito ku nyumba za mtsogoleri wa dziko, Prince Kapondam’gaga kuti akhale mmaso kamba koti pali anthu ena omwe akungofuna kumudyera.

Chenjezoli labwera kutsatira mphekezera zomwe zamveka kuti a Kapondam’gaga awonetsa chidwi chofuna kudzapikisana nawo pa mpando wa mtsogoleri wa chipanichi patsogolo pa chisankho cha dziko lino mu 2030.

Poyankhula pakanema wina mmodzi mwa akatswiri pa ndale, Bishop Chimwemwe Chafumuka anati sakukhulupira kuti a Kapondam’gaga akhoza kufuna mpandowu potengera kuti ankagwira ntchito ndi a Chakwera pomwe anthu anadana ndi ulamuliro wa MCP.

“Sindikukhulupira kuti akufunadi kuyima. Asaganize, akudzilakwira ndipo anthu omwe akuwadyera ndalama a Kapondam’gaga akuwalakwira” anatero Chafumuka.

Chafumuka anapitiriza kuti a Chakwera ankanenedwa kuti anatenga anthu akumpingo kwawo kulemba ntchito ndipo ena mwa iwo ndi a Kapondam’gaga, zomwe akuwona kuti mkuluyu anali anali mbali imodzi yakulephera kwa ulamuliro wa MCP.

Iwo anati akukhulupira kuti a Kapondam’gaga akupopedwa ndi anthu omwe akungowadyera, kapena wolemba nkhani kapenaso anthu ena omwe akungofuna kuwayika patsogolo posafuna kuti padzakhale mpikisano wa mphamvu mchipanichi.

Kumbali yake wolemba nkhani odziwika kwambiri, Bright Mhango anati mwina chidwi cha a Kapondam’gaga chabwera poti ndi munthu yemwe anakhala kwambiri pafupi ndi a Chakwera ndipo akudziwa kwambiri zofooka zawo.

Mhango anati, potengera kuti ulamuliro wa MCP unalephera a Chakwera ndi Kapondam’gaga ali ndi mphamvu mu ulamuliro, anapempha kuti nawoso a Chakwera abwere poyera ndikuyankhulapo pa nkhaniyi.

“Tamva kuti a Kapondam’gaga akumayenda ndikumanena zofooka za a Chakwera, nawoso a Chakwera akanabwera poyera ndikufotokoza mbali yawo, mwina sankachita bwino anali a Kapondam’gaga wo ndicholinga chofuna kudzapeza danga lokhalira mtsogoleri wa chipanichi” anatero Mhango.

Pakadali pano a Lazarus Chakwera sanabwere poyera ndikuyankhula ngati adzapikisane nawo pa chisankho cha chipanichi kapena ayi.

Ma ripoti akuwonetsa kuti malamulo a MCP sakuwalora a Chakwera kudzayima kamba koti nthawi yokhala mtsogoleri wachipanichi inadutsa, koma malamulo a dziko lino akuwalola kudzapikisana nawo ngati mtsogoleri wa dziko.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading