Mega Farms Loan Recovery – Urgent Maize Delivery

ATTENTION: ALL MEGA FARMS BENEFICIARIES WITH OUTSTANDING LOANS
The Ministry of Agriculture, Irrigation and Water Development and Malawi Agricultural and Industrial Investment Corporation plc (MAIIC) hereby reminds all Mega Farms beneficiaries with outstanding loans to MAIIC who are holding maize stocks under the Mega Farms project to arrange for the delivery of the maize to the designated ADMARC, National Food Reserve Agency (NFRA) and Agricultural Commodity Exchange for Africa (ACE) depots listed below by November 22, 2026.
Maize deliveries are intended to facilitate the recovery of outstanding loans owed under the Mega Farms project. All affected farmers are therefore urged to deliver their maize in accordance with their applicable loan repayment obligations and the relevant delivery arrangements.
CHIDZIWITSO KWA ALIMI A NGONGOLE ZA MEGA FARMS KUITANA KWA ALIMI KUTI APEREKE CHIMANGA CHOLOWA M’NGONGOLE
Unduna wa Zaulimi, Mthilira ndi Chitukuko cha Madzi ndi kampani ya Malawi Agricultural and Industrial Investment Corporation plc (MAIIC) likudziwitsa alimi onse amene analandira ngongole kudzera mu ndondomeko ya Mega Farms ndipo ali ndi ngongole zomwe sanamalize kubweza, komanso omwe akusungabe chimanga chomwe chinapezeka kudzera mu ndondomekoyi, kuti akonze mwamsanga zopereka chimangacho ku madepoti a ADMARC, National Food Reserve Agency (NFRA) ndi Agricultural Commodity Exchange for Africa (ACE) omwe atchulidwa pansipa pasanafike pa November 22, 2026.
Cholinga cha kupereka chimangachi ndi kuthandiza kubweza ngongole zomwe alimi ali nazo pansi pa ndondomeko ya Mega Farms. Choncho, alimi onse okhudzidwa akuyenera kupereka chimanga chawo motsatira zomwe anagwirizana pa ngongole zawo komanso dongosolo lovomerezeka la kaperekedwe ka chimanga.
DESIGNATED DELIVERY DEPOTS / MADEPOTI OKASIYAKO CHIMANGA
ADMARC DEPOTS / MADEPOTI A ADMARC
Mzimba Boma, Rumphi Boma, Salima Boma, Kasungu Main, Chatoloma, Santhe, Mponela, Nkhwazi, Mkanda, Chilambula, Mzuzu
NFRA DEPOTS / MADEPOTI A NFRA
Kanengo, Mzuzu, Mangochi, Luchenza
AGRICULTURAL COMMODITY EXCHANGE FOR AFRICA (ACE) — DEPOTS / MADEPOTI
Nathenje, Lilongwe; Kapirimutu, Dedza; Gwiritse, Lilongwe; Naphini, Lilongwe; Chikwatula, Ntchisi; Mgwirizano, Dowa; Chilimika, Salima; Kasipa, Nkhotakota; Chilanga, Kasungu; Tasanganapo, Mzimba; Vikuyu, Kasungu; Machichi, Mchinji; Nabulenje, Mchinji; Msungawanthu, Dowa; Jumabunguzi, Salima; Balaka NASFAM, Balaka; Mulanje NASFAM, Mulanje; Phalombe NASFAM, Mzimba; Mwandama, Zomba; Jenda NASFAM, Mzimba
IMPORTANT NOTICE ON NON-COMPLIANCE
Farmers who fail to deliver the required maize or otherwise meet their applicable repayment obligations may be referred to debt collectors and may face legal proceedings for recovery of the outstanding amounts, together with any applicable costs, interest or other amounts recoverable under their loan agreements and the law.
All affected farmers are urged to act promptly to avoid further recovery action. Farmers who require clarification regarding their outstanding balances or delivery obligations should contact MAIIC immediately.
CHENJEZO LOKHUDZA KUSAPEREKA CHIMANGA
Alimi amene alephera kupereka chimanga chofunika kapena kulephera kukwaniritsa udindo wawo wobweza ngongole angatumizidwe kwa anthu kapena makampani osonkhanitsa ngongole. Komanso, MAIIC ingayambe milandu kukhoti pofuna kubweza ngongole zomwe zatsala, kuphatikizapo ndalama zina zilizonse, chiwongola dzanja kapena ndalama za milandu zomwe zingathe kulipiritsidwa mwalamulo komanso malinga ndi mapangano a ngongole.
Alimi onse okhudzidwa akulimbikitsidwa kuchitapo kanthu mwamsanga kuti apewe njira zina zobwezera ngongole. Alimi amene akufuna kudziwa ndalama zomwe ali nazo zotsala pa ngongole kapena njira yoyenera yoperekera chimanga chawo alumikizane ndi MAIIC mwamsanga.
Telephone: +265 884 030 115
Email: [email protected]