Fisi anakana msatsi! Wakanitsitsa mlembi wamkulu ku chipani cha Malawi Congress (MCP) Richard Chimwendo Banda kuti iye ndiyemwe adapangitsa kuti chipanichi chizepulidwe pa zisankho za chaka chatha, ndipo wati siyani kumuloza chala.
Chimwendo Banda wayankhula izi Lachiwiri madzulo pomwe amacheza ndi imodzi mwa nyumba zofalitsa nkhani komwe wati iye adachita mbali yake limodzi ndi a Lazarus Chakwera kumemeza anthu mokwanira.
Iye wati anamemeza anthu kukalembetsa komanso kukavota, koma aMalawi ambiri anatengeka ndi kukhulupirira mabodza a ena m’malo moti afatse ndikudziwa zenizeni.
Chimwendo Banda wati mtsogoleri wachipani chawo Chakwera amkamanga misewu, nyumba za achitetezo mwa zina koma aMalawi anayiwala ndi kukhulupilira mfundo zoti ena amkadya chitedze pa nthawiyo.
Iwo ati pa nthawiyo anthu amkadya Kalongonda osati chitedze.
Pomwe anthu ena mchipani cha MCP akuti mlembi wamkuluyu atule pansi udindo limodzi ndi a Chakwera, iwo ati chipani chirichonse sichilephera kukokana ndi kutsutsana pa zinthu koma ulemu ndi ofunika.
“Pasamapezeke munthu otukwana mzako koma kunena mfundo zogwira mtima” watero Chimwendo Banda.
Chimwendo watinso ngati anthu adzafune a Chakwera kuti akapikisane nawo pa mpando wa mtsogoleri wa dziko pansi pa mbendera ya MCP, mzosavuta kukasintha malamulo omwe pano akuwakaniza kuyimiranso.
Pa nkhani za ndalama zomwe ofuna kupikisana nawo pa mipando ya kuchipani mmadera akuyenera kupereka, Banda wati mtsogoleri wa chipanichi anayimitsa kaye ndondomekoyo.
Iwo ati koma pokhala mkulu wa chipanichi, zolakwika zonse zimaloza iwo.
Posachedwapa pa msonkhano wa achinyamata a chipanichi kwa Nsundwe m’boma la Lilongwe, mfundo zidaphulika kuti a Chimwendo Banda atule pansi udindo ponena kuti akusokoneza chipanichi ndipo adachilepheretsa masankho.
M’modzi mwa ma membala ake a George Kaunda adati a Banda akusokonezanso pobweretsa ndondomeko yoti opikisana nawo ku chipanichi adziripira ndalama zomwe phungu wa chipanichi a Lawrence Chakakala Chaziya anagwirizana nazo kuti pakulakwika.