Ngati munataya chikhulupiliro, boma likuti osapanga za nguluwe yolira msampha utaning’a, pomwe lati kwangotsala kanusu chabe kuti mavuto omwe akuta dziko lino athe.
Nduna yofalitsa nkhani, Shadric Namalomba wati ndiwokhudzika ndi nyengo zomwe a Malawi akudutsamo monga kusowa kwa mafuta, ndalama zakunja ndi kuvuta kwa magetsi, koma wati anthu asataye mtima pomwe wati mavutowa pompano akhala mbiri ya make dzana.
Poyankhula pa wayilesi ya kanema ya Zodiak loweruka, Namalomba wati utsogoleri umayenera kuchita zinthu zokomera mzika nthawi zonse osati kupanga zinthu pongofuna mavoti pa chisankho cha 2030
“Eya tikudera nkhawa komaso ndife okhudzika kamba koti mavutowa akukhudza ufulu wa a Malawi, tikungoyenera kupanga zolondola” anatero atafusidwa ngati akudera nkhawa komaso kukhudzika ndimavutowa.
A Namalomba ati ayimabe pa mau a mtsogoleri wa dziko lino kuti zinthu zidzayamba kuyenda zikatha zaka ziwiri ndipo pa dakali pano ndili mu chaka chachiwiri kuchokera pa 16 September chaka chino.
Iwo ati ankaganiza kuti athana ndi vuto lakusowa kwa ndalama zakunja mwachangu koma zitengabe kanthawi popeza pomwe DPP inkalowa m’boma inapeza ndalama zakunja zamasiku khumi okha koma pano njira zili mkati zofuna kuthana ndi vutoli monga kuchepetsa kugula katundu kunja, kulimbikitsa ulimi ndi zamigodi zomwe zizigulitsidwa kunja.
Kumbali yamagetsi, Namalomba wati boma lawo likuyesetsa kuthana ndikuzimazima kwamagetsi pogula zipangizo zothandizira kuwonjezera mphavu ndipo posachedwapa vuto iliso likhala mbiri chabe.
Nduna yazofalitsa ma uthengayi, yati ngakhale pali zovuta zina koma boma la DPP lachita bwino kumbali yopereka ndalama ya CDF, kuwonetsetsa kuti sukulu zikhale za ulere, kuchepetsa kukwera mtengo kwa katundu komaso kuti chakudya chidzipezeka.