Civil sitimu ya mphamvu kuti timasowa nayo mtendere – Chikhosi


Shadreckchikhosi- Malawi24
Mphunzitsi wa timu ya Silver Strikers Ladies, Shadreck Chikhosi wati Civil Women yangochita mwayi kuti yawagonjetsa lero mu NBM Women’s Premiership koma atsikana a m’bomawa sikuti ndi a mphamvu zoti zingawasowetse mtendere kunkhani yolimbirana ukatswiri.

Chikhosi amayankhula izi atangotha masewero omwe timu yake yafa ndizigoli zitatu kwa ziwiri mmanja mwa Civil pa bwalo la Silver loweruka.

“Awa mwati timalimbirana nawo ukatswiri koma sikuti timalimbirana nawo, iyi sitimu yamphamvu kuti timasowa nayo mtendere kungoti lero yachita mwayi kuti yapambana” anatero Chikhosi atafusidwa ndi wolemba nkhani kuti athirepo ndemanga pakugonja kwawo ndi team ya Civil yomweso imakhala mu gulu lolimbirana ukatswiri.

Civil Women inatsogola pa mphindi 18 kudzera mwa Mercy Vitumbiko Mkandawire ndipo katswiriyu anabwereso ndi chigoli china pa mphindi 42 kuti masewero akhale 2 kwa duuu.

Ma Banker akaziwa anadzambatuka mu nthawi yowonjezera mchigawo choyambachi kudzera mwa Madina Ngulube kuti chigawo choyamba chithere 2-1 kukomera alendo.

Meneni Kapasule analowa kuchokera panja mchigawo chachiwiri ndikukawonjezera ululu pachilonda cha Silver Ladies pomwe anagoletsa pa mphindi 71 kuti ikhale 3-1.

Silver Strikers inabweraso kudzera mwa Ireen Khumalo yemwe anagoletsa mu mphindi 77 koma sizinali zokwana kuti ipeze kalikonse mmasewerowa mpaka woyimbira anathetsa, kutsimikiza kuti Civil Service Women ndiyo mfumu ya mzinda wa Lilongwe.

Koma ngakhale ma Banker agonja koma Chikhosi ananenetsa kuti timu yake iteteza ukatswiriwu.

Mphunzitsi wa Civil Service Women, Collins Pofera wati ndiwokondwa kuti malingaliro ofuna kulimbirana ukatswiri wa chaka chino akuwoneka.

“Atsikana awonetsa mtima ofuna kulimbirana nawo ukatswiri wa chaka chino. Ndiwayamike ndi mmene achitira lero” anatero Pofera.

Zateremu Civil Women’s yabwera pamwamba pa mndandanda wamatimu mu chikhochi pomwe tsopano ili ndi mapoint 9 pamasewero anayi. Timuyi yakhala pamwamba kamba kogoletsa zigoli zambiri kuposa FCB Nyasa Big Bullets Women yomwe ndiyachiwiri komaso Silver Strikers Ladies yomwe ndiyachutatu, ngakhale onsewa ali ndi ma point ofanana.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading