Boma likugula ma lona K30 miliyoni imodzi


61bmrnhkudl Ac Uf10001000 Ql80- Malawi24

Azizidwa a Malawi atava kuti boma kudzera ku bungwe la ADMARC likufuna kugula ma lona 100 oyanikira za kumunda pa mtengo wa K30 miliyoni imodzi.

Nkhaniyi yadziwika pomwe bungwe la ADMARC lalengeza kuti lapereka kuntalakiti ya ndalama zokwana K3 biliyoni ku kampani ya Maiden Investments kuti igule malonawa omwe pachizungu akutchedwa Tarpaulin.

Mtengo wa kuntalakitiyi ukutanthauza kuti lona imodzi izigulidwa pa mtengo wapafupifupi K30 million.

Pakadali pano, a Malawi ochuluka asonyeza kukaikira ngati mitengoyi ili ya chilungamo ndipo ena akuti mkofunika kuti kuntalakitiyi iyimitsidwe kaye

Mmodzimwa a Malawi okhumudwa ndi nkhaniyi ndi a Stanley Onjezani Kenan, omwe ndiodziwika bwino pa masamba anchezo.

A Kenan sanapsatire mawu. Iwo akuti payenda umbamva pa kuntalakitiyi.

“Abale, ma tarpaulin odula chonchi ndi a mtundu wanji? Ma tarpaulin akulu kwambiri a 60ft x 40ft ali pa K5.6 miliyoni kuphatikizapo VAT., 750gsm thickness yake.

“Pa ma tarpaulin 100 siikanadutsa K560 miliyoni. Ndiye mpaka K3 biliyoni mmmm, kuba kopanda nako manyazi.,” wadabwa Kenan kudzera pa tsamba lake la fesibuku.

Pakadali pano, bungwe la ADMARC silinabwere poyera ndikufotokoza bwino za kuntalakitiyi.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading